Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizilimbikitsa Anthu Achidwi Kuti Azifika Kumisonkhano Yathu

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizilimbikitsa Anthu Achidwi Kuti Azifika Kumisonkhano Yathu

N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA? Nthawi ya misonkhano timakhala ndi mwayi ‘woimbira Yehova’ komanso ‘kumutamanda.’ (Sal. 149:1) Timaphunziranso zimene tingachite kuti tizichita zimene Yehova amafuna. (Sal. 143:10) Ngati anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akufika pamisonkhano amadziwa zinthu zochuluka komanso amayamba kukonda kwambiri Yehova.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muziitana munthu ngakhale pa ulendo woyamba. Simuyenera kudikira kuti muyambe kuphunzira naye Baibulo kuti mudzamuitanire kumisonkhano.—Chiv. 22:17

  • Mukakumana ndi munthu wachidwi, mufotokozereni zimene zimachitika kumisonkhano yathu komanso zimene tidzaphunzire mlungu wotsatira. Mungagwiritse ntchito kapepala koitanira anthu kumisonkhano, vidiyo yakuti, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?, kapena mungakambirane naye mutu 5 ndi 7 m’kabuku kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

  • Mungachite bwino kumuthandiza kudziwa zovala zoyenera zomwe angavale kumisonkhano komanso kukamutenga kuti mupitire limodzi ku Nyumba ya Ufumu. Mukafika ku Nyumba ya Ufumu, muzikhala naye pafupi kuti muziona limodzi mabuku athu. Mungachitenso bwino kumuthandiza kuti adziwane ndi abale ndi alongo