Akulalikira kwa mayi ndi mwana wake ku West Bengal m’dziko la India

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU September 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Onani zitsanzo za Ulaliki wa magazini a Nsanja ya Olonda ndi mfundo ya m’Baibulo yomwe imasonyeza kuti Mulungu amatiganizira. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’

Kodi kutsatira chilamulo cha Yehova kumatanthauza chiyani? Munthu amene analemba Salimo 119 ndi chitsanzo chabwino kwa ife masiku ano.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira

Kodi tingantani ngati tapeza mwana pakhomo lomwe tikufuna kulalikira? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza udindo wa makolo ake?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Thandizo Langa Lichokera kwa Yehova”

Salimo 121 limafotokoza mmene Yehova amatithandizira komanso kutitetezera.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tinapangidwa Modabwitsa Kwambiri

Mu Salimo 139, Davide analemba zokhudza mmene Yehova anatilengera modabwitsa.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zinthu Zimene Tiyenera Kupewa Tikamachititsa Phunziro la Baibulo

Kodi tingatani ngati tikufuna kuti tiziwafika pamtima anthu amene timaphunzira nawo Baibulo?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Yehova ndi Wamkulu ndi Woyenera Kutamandidwa Kwambiri”

Salimo 145 limasonyeza kuti Davide ankadziwa kuti Yehova amasamalira atumiki ake okhulupirika.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizilimbikitsa Anthu Achidwi Kuti Azifika Kumisonkhano Yathu

Anthu amene timaphunzira nawo Baibulo komanso anthu ena achidwi angapindule kwambiri ngati atamafika pamisonkhano.