Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | HOSEYA 1-7

Kodi Mumasangalala ndi Chikondi Chokhulupirika Ngati Mmene Yehova Amachitira?

Kodi Mumasangalala ndi Chikondi Chokhulupirika Ngati Mmene Yehova Amachitira?

Chikondi chokhulupirika chimatanthauza kudzipereka, kukhulupirika komanso kukonda winawake ndi mtima wonse. Pofuna kutiphunzitsa za chikondi chimenechi komanso kukhululuka, Yehova anagwiritsa ntchito zimene zinachitikira Hoseya ndi mkazi wake wosakhulupirika Gomeri.​—Hos. 1:2; 2:7; 3:1-5.

Kodi Gomeri anasonyeza bwanji kuti analibe chikondi chokhulupirika?

Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti analibe chikondi chokhulupirika?

Kodi Hoseya anasonyeza bwanji Kuti anali ndi chikondi chokhulupirika?

Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikondi chokhulupirika?

FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi ndingamusonyeze bwanji Yehova chikondi chokhulupirika?