Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Tikuphunzira Kuchokera m’Buku la Yona

Zimene Tikuphunzira Kuchokera m’Buku la Yona

Yehova anachititsa kuti nkhani zosiyanasiyana za amuna ndi akazi okhulupirika zilembedwe m’Mawu ake n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu. (Aroma 15:4) Kodi mwaphunzira zotani m’buku la Yona? Onerani vidiyo yakuti Kulambira kwa Pabanja: Yona Anaphunzira Kuti Mulungu Ndi Wachifundo, kenako yankhani mafunso otsatirawa:

  • Kodi ofalitsa atatu a m’vidiyoyi anakumana ndi mavuto otani?

  • Kodi mfundo za m’buku la Yona zingatithandize bwanji tikapatsidwa uphungu kapena tikauzidwa kuti tisiye kuchita utumiki winawake? (1 Sam. 16:7; Yona 3:1, 2)

  • Kodi nkhani ya Yona ingatithandize bwanji kuti tiziwaona moyenerera anthu a m’gawo lathu? (Yona 4:11; Mat. 5:7)

  • Kodi zimene zinachitikira Yona zingatithandize bwanji ngati tikudwala matenda aakulu? (Yona 2:1, 2, 7, 9)

  • Kodi mwaphunzira zotani m’vidiyoyi zomwe zikusonyeza kuti kuwerenga Baibulo komanso kuganizira zimene tawerengazo n’kofunika kwambiri?