Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AMOSI 1-9

‘Yesetsani Kufunafuna Yehova Kuti Mupitirize Kukhala ndi Moyo’

‘Yesetsani Kufunafuna Yehova Kuti Mupitirize Kukhala ndi Moyo’

5:6, 14, 15

Kodi kufunafuna Yehova kumatanthauza chiyani?

  • Kumatanthauza kupitiriza kuphunzira za iye komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wathu

Kodi chinkachitika n’chiyani Aisiraeli akasiya kufunafuna Yehova?

  • Ankasiya ‘kudana ndi zoipa ndipo sankakonda zabwino’

  • Ankayamba kuchita zinthu zongodzisangalatsa okha

  • Ankasiya kutsatira malamulo a Yehova

Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti pofuna kutithandiza kuti tizimufunafuna?