Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Achinyamata Musachedwe Kulowa ‘Pakhomo Lalikulu’

Achinyamata Musachedwe Kulowa ‘Pakhomo Lalikulu’

Mukhoza kumaganiza kuti mudzakhala wachinyamata mpaka kalekale ndiponso kuti simudzakumana ndi mavuto amene amabwera chifukwa chokalamba. (Mlal. 12:1) Ngati ndinu wachinyamata, kodi mumaona kuti muli ndi nthawi yambiri moti mukhoza kudikira kaye musanakwaniritse zolinga zanu potumikira Yehova?

Kumbukirani kuti “zinthu zosayembekezereka zimagwera” tonsefe, kuphatikizapo achinyamata. (Mlal. 9:11) Komanso “simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.” (Yak. 4:14) Choncho musachedwe kukwaniritsa zolinga zanu potumikira Yehova popanda zifukwa zomveka. Lowani ‘pakhomo lalikulu la mwayi wautumiki’ lidakali lotseguka. (1 Akor. 16:9) Mukachita zimenezi, simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.

Zolinga zina zimene mungakhale nazo:

  • Kuphunzira chinenero china kuti muzilalikira anthu achinenerocho

  • Kuchita upainiya

  • Kupita kusukulu yophunzitsa Baibulo

  • Kugwira nawo ntchito zomangamanga

  • Kutumikira pa Beteli

  • Kukhala woyang’anira dera

Lembani zolinga zanu: