Pitani ku nkhani yake

Malangizo a Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Malangizo a Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

1. Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu uzichitika motsatira malangizo amene ali mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso amene ali papepala la malangizo lino. Ofalitsa onse akuyenera kulimbikitsidwa kuti alembetse n’cholinga choti azipatsidwa nkhani za ophunzira. Anthu enanso amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse ndipo amatsatira mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa komanso mfundo zachikhristu pa moyo wawo, angalembetse kuti azipatsidwa nkhani za ophunzirazi.​—be tsa. 282.

  2. 1 miniti. Mlungu uliwonse, pambuyo pa nyimbo yoyamba komanso pemphero, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azifotokoza mwachidule zimene tiphunzire. Tcheyamaniyo azitsindika kwambiri mfundo zimene abale ndi alongo angapindule nazo kwambiri.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  3. Nkhani: 10 minitsi. Pa Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu pazikhala mutu komanso mfundo zikuluzikulu ziwiri kapena zitatu. Nkhaniyi iyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Tikamayamba buku latsopano la m’Baibulo, tizionera vidiyo. Ndiyeno wokamba nkhaniyo azisonyeza kugwirizana pakati pa vidiyoyo ndi mutu umene uli mu kabuku. Koma ayeneranso kuonetsetsa kuti wafotokoza mfundo zimene zili m’kabukuko. Komanso ngati nthawi ilipo, ayenera kufotokozera zithunzi zimene zaikidwa zomwe zimakonzedwa kuti zithandize kumveketsa mfundo za mʼnkhaniyo. Akhozanso kuonjezera malifalensi ena amene akuthandiza kumveketsa bwino mfundo za mʼnkhani yake.

 4. Mfundo Zothandiza: 10 minitsi. Iyi ndi nkhani ya mafunso ndi mayankho yopanda mawu oyamba ndiponso omaliza. Nkhaniyi izikambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Iye ayenera kufunsa mafunso onse awiri. Komanso, akhoza kusankha kuwerenga mavesi onse amene aikidwa kapena ayi. Anthu amene atchulidwa kuti ayankhe ayenera kufotokoza ndemanga zawo kwa nthawi yosapitirira masekondi 30.

 5. Kuwerenga Baibulo: 4 minitsi. Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale. Ayenera kungowerenga mavesi amene wauzidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Tcheyamani ayenera kuthandiza munthuyo kuti amvetse zimene akuwerenga, awerenge molondola komanso mosadodoma, azisintha mawu, kupuma moyenera ndiponso kulankhula mwachibadwa. Popeza kuti mavesi ena amene abale azipatsidwa kuti awerenge azikhala ambiri ndipo ena azikhala ochepa, woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu ayenera kuganizira luso la wophunzira akamagawa nkhani zimenezi.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 6. 15 minitsi. Chigawo chimenechi cha msonkhano chakonzedwa kuti chizithandiza aliyense kuyeserera zimene angachite mu utumiki komanso kuwonjezera luso lolalikira ndi kuphunzitsa. Ofalitsa azikambirana zitsanzo za ulaliki zimene zikupezeka mu Kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Komabe, ngati palibe malangizo achindunji, ofalitsa angasankhe kufunsa funso, lemba, linki kapena kuonetsa vidiyo, kugawira buku kapena kabuku kuchokera pa Zinthu Zophunzitsira kapena kuchita chitsanzo cha ulaliki chimene chingathandize mʼderalo. Pofuna kutithandiza tikakhala mu utumiki, pa mbali yakuti Zimene Tinganene pali mawu otithandiza kudziwa kumene lembalo likupezeka m’mabuku amene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu. Ophunzira angasankhe ngati akufuna kugwiritsa ntchito mbali imeneyi m’nkhani yawo kapena ayi. Pa Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu pali nthawi imene nkhani iliyonse ya ophunzira iyenera kukambidwa ndipo nthawi zina pandandandayi pangakhalenso malangizo ena owonjezera. Ophunzira sakuyenera kuwonjezera mfundo zina pa nkhani imene apatsidwa n’cholinga choti angomaliza nthawi yawo yonse. Kumbukirani kuti zitsanzo zina zokonzedwa bwino zikhoza kutha kutatsala miniti imodzi kapena maminitsi angapo. Akulu angapatsidwe nkhani za ophunzira, ngati pakufunika kutero. Nthawi zina, pa gawo limeneli padzaikidwa vidiyo imene idzakhale yokambirana mʼmalo mwa vidiyo ya zimene tinganene mu utumiki. Zikatero, mbali imeneyi iyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera.

 7. Mavidiyo a Zimene Tinganene mu Utumiki: Nthawi ndi nthawi, tizionera ndi kukambirana mavidiyo a zimene tinganene mu utumiki. Mavidiyowa azikhala a zitsanzo za ulendo woyamba ndi maulendo obwereza. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi amene azitsogolera mbali imeneyi.

 8. Ulendo Woyamba: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale kapena munthu wa m’banja lake. Mwininkhani pamodzi ndi mwininyumba angasankhe kukhala pamipando kapena kuimirira, ndipo angapatsane moni wogwirizana ndi chikhalidwe cha kuderalo. Pokamba nkhani yawoyi, agwiritse ntchito mfundo za pa chitsanzo cha zimene tinganene mu utumiki zomwe zili mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

 9. Ulendo Wobwereza: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale. (km 5/97 tsa. 2) Onse angakhale pamipando kapena kuimirira pamene akukamba nkhaniyi. Wophunzirayo asonyeze zoyenera kulankhula kwa munthu amene anasonyeza chidwi paulendo woyamba. Pokamba nkhani yawoyi, agwiritse ntchito mfundo za pa chitsanzo cha zimene tinganene mu utumiki zomwe zili mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

 10. Phunziro la Baibulo: Nkhaniyi iperekedwe kwa m’bale kapena mlongo. Ngati yaperekedwa kwa mlongo, mwininyumba akhalenso mlongo ndipo ngati yaperekedwa kwa m’bale, mwininyumba akhalenso m’bale. (km 5/97 tsa. 2) Onse angakhale pamipando kapena kuimirira pamene akukamba nkhaniyi. Nkhaniyi izisonyeza phunziro la Baibulo lomwe layamba kale kuchitika. Palibe chifukwa chokhala ndi mawu oyamba kapena omaliza, pokhapokha ngati mutu wa phunziro limene wophunzirayo wapatsidwa ukunena zimenezo. Sizofunika kuwerenga ndime zonse zimene mwapatsidwa, ngakhale kuti mungasankhe kuwerenga. Wokamba nkhaniyi akufunika kusonyeza luso labwino kwambiri lophunzitsa.

 11. Nkhani: Nkhaniyi iziperekedwa kwa m’bale basi ndipo aziikamba yekha mofanana ndi nkhani zina zokambidwa pa mpingo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 12. Nyimbo ikatha, 15 minitsi yotsatira ya chigawochi izikhala ndi nkhani imodzi kapena ziwiri zothandiza anthu kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu pamoyo wawo. Nkhanizi zingaperekedwe kwa akulu kapena atumiki othandiza oyenerera. Koma ngati ndi zofunika pampingo ziyenera kukambidwa ndi akulu okha. Abale amene apatsidwa nkhani zokambirana ndi omvera azifotokoza mawu oyamba mwachidule. Ngati nkhani ikupezeka mu Kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, m’bale amene akukamba nkhaniyo angagwiritsire ntchito mafunso owonjezera pofuna kumveketsa mfundo inayake mu nkhaniyo.

 13. Phunziro la Baibulo la Mpingo: 30 minitsi. Iperekedwe kwa mkulu woyenerera. (M’mipingo yomwe akulu ndi ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapatsidwe mbali imeneyi ngati pakufunika kutero.) Bungwe la akulu likuyenera kuunika luso lophunzitsa la mkulu aliyense kuti lisankhe akulu amene ali oyenerera kuchititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Akulu amene angasankhidwewo akuyenera kuchititsa phunziroli mogwira mtima, kuthandiza omvera kuti atulutse mfundo zothandizadi pa malemba oyenerera, kuthandiza aliyense kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’phunziroli pa moyo wake, ndipo sayenera kudya nthawi. Abale amene asankhidwa kuti azichititsa phunziroli akuyenera kuwerenga ndi kutsatira mfundo zimene gulu lafalitsa zokhudza mmene tingachititsire Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ngati mwamaliza kukambirana mfundo zonse za nkhani ya mlunguwo, palibe chifukwa chotalikitsira phunzirolo pongofuna kumaliza nthawi imene yatsala. Ngati zili zotheka, mlungu uliwonse Phunziro la Baibulo la mpingo lizichititsidwa ndi m’bale wina ndipo m’bale winanso aziwerenga ndime, osati m’bale amene anawerenga mlungu wapita. Ngati tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu wanena kuti phunziroli lichitike mwachidule chifukwa cha nthawi, m’bale amene akuchititsa phunziroli azisankha yekha mmene angalichititsire mwachidule. Iye akhoza kusankha kuti ndime zina zisawerengedwe koma angofunsa mafunso.

MAWU OMALIZA

  14. 3 minitsi. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azibwereza mwachidule mfundo zothandiza zimene taphunzira pa msonkhanowo. Azitchulanso mwachidule zimene tidzaphunzire mlungu wotsatira. Ngati nthawi ilipo angatchule mayina a anthu amene apatsidwa nkhani mlungu wotsatira. Tcheyamani akhozanso kupereka zilengezo zofunika kapena kuwerenga makalata pa nthawi imeneyi. Zilengezo za nthawi zonse, monga zokhudza kulowa mu utumiki wa kumunda kapena kuyeretsa Nyumba ya Ufumu sizikuyenera kulengezedwa koma zizingoikidwa pabolodi la mpingo. Ngati zilengezo n’zambiri kapena kalata ndi yaitali ayenera kupeza nthawi kapena kupempha abale a nkhani pa gawo lakuti Moyo Wathu Wachikhristu, kuti azifupikitse. (Onani ndime 13 ndi 17.) Msonkhanowu uzitha ndi nyimbo ndi pemphero.

KUWERENGA KOMANSO KUPHUNZITSA MWALUSO

 15. Wophunzira aliyense azibweretsa kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso kaya kosindikizidwa kapena pa chipangizo chamakono. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azigwiritsa ntchito kabukuka poyamikira ndiponso kupereka malangizo kwa ophunzira. Wophunzira aliyense azigwiritsa ntchito phunziro limene lili mumkutiramawu pa nkhani imene wapatsidwa pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Gawo lakuti “Zimene Inuyo Mwachita” la kabukuka lakonzedwa n’cholinga choti wophunzira aziligwiritsa ntchito, choncho tcheyamani sakuyenera kulembapo chilichonse.

KUYAMIKIRA NDIPONSO KUPEREKA MALANGIZO

  16. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu azimuyamikira ndiponso kumupatsa malangizo kwa nthawi yosapitirira 1 miniti, ndipo malangizowo azichokera m’kabuku ka Kuphunzitsa. Tcheyamani akatchula nkhani imene wophunzira akukamba, asatchulenso phunziro limene wapatsidwa. Koma akamaliza, tcheyamaniyo ayenera kumuyamikira ndipo angatchule phunziro limene anapatsidwa, kufotokoza mbali imene wachita bwino kapena zimene ayenera kusintha ulendo wotsatira. Tcheyamani angasankhenso kuyamikira kapena kupereka malangizo pa mbali zina zokhudza mmene wophunzirayo wakambira nkhani yake ngati akuona kuti zingathandize wophunzirayo kapena omvera. Tcheyamani angaperekenso malangizo othandiza kwa wophunzira misonkhano ikatha kapena tsiku lina ndipo malangizowo ayenera kuchokera m’kabuku la Kuphunzitsa kapena buku la Sukulu ya Utumiki. Malangizowo angachokere pa phunziro limene wophunzirayo anapatsidwa kapena pa phunziro lina.​—Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya udindo wa tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso udindo wa mlangizi wothandiza, onani  ndime 17,  22, ndi  23.

KUSUNGA NTHAWI

   17. Mbali iliyonse komanso ndemanga za tcheyamani zisapitirire nthawi yake. Ngakhale kuti nthawi imene yaperekedwa pa nkhani iliyonse sinasonyeze mwachindunji kuti “ kapena osapitirira,“ palibe chifukwa chopitirizira kukamba nkhani ngati mfundo zonse zafotokozedwa bwino nthawi yoikidwa isanakwane. Nkhani za ophunzira ziziimitsidwa mwaluso nthawi yake ikatha. Ngati mbali zina zapitirira nthawi, mlangizi wothandiza azipereka malangizo kwa munthuyo pambali. (Onani  ndime 23.) Msonkhano wonse kuphatikiza nyimbo ndi pemphero zisapitirire ola limodzi ndi 45 minitsi.

WOYANG’ANIRA DERA AKAMACHEZERA MPINGO

 18. Woyang’anira dera akamachezera mpingo, mapulogalamu aziyenda mmene tasonyezera mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Koma nkhani yautumiki imene woyang’anira dera amakamba kwa 30 minitsi izilowa m’malo mwa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Nkhani yautumikiyo isanayambe, tcheyamani ayenera kubwereza zimene taphunzira, kutchula pang’ono zimene tiphunzire mlungu wotsatira, kulengeza zinthu zofunika, kuwerenga makalata ngati alipo kenako kuitana woyang’anira derayo kuti adzakambe nkhani yake. Woyang’anira derayo akamaliza nkhani yake adzauza anthu kuti aimbe nyimbo yomaliza imene iye wasankha. Angathe kupempha m’bale wina kuti adzatseke ndi pemphero. Kalasi B ya m’chinenero cha mpingowo sikuyenera kuchitika pa mlungu umene woyang’anira dera akuchezera mpingo. Koma kagulu kayenera kuchitabe misonkhano yake ngakhale kuti woyang’anira dera akuchezera mpingo umene umathandiza kaguluko. Koma pa nthawi imene woyang’anira dera akukamba nkhani yautumiki, kaguluko kakuyenera kumvetsera nkhaniyo.

MLUNGU WA MSONKHANO WADERA KAPENA WACHIGAWO

 19. Ngati muli ndi msonkhano wadera kapena wachigawo, misonkhano yampingo ya mlunguwo siyenera kuchitika. Muyenera kuphunzira mfundo za pa misonkhano ya mpingoyo pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira panokha.

MLUNGU WA CHIKUMBUTSO

 20. Misonkhano ya mpingo ya mkati mwa mlungu sikuyenera kuchitika ngati tsiku la Chikumbutso lilinso mkati mwa mlungu. Komabe, msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda ukuyenera kuchitika patsiku la Chikumbutso.

WOYANG’ANIRA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 21. Bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu mmodzi kuti akhale woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Iye azionetsetsa kuti msonkhanowu ukuchitika mwadongosolo komanso motsatira malangizo amene tafotokozawa. Ayeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi mlangizi wothandiza. Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu kakangofika, iye ndi amene azigawa nkhani zonse za misonkhano ya mkati mwa mlungu kwa miyezi iwiri. (Onani  ndime 2-14.) Zimenezi zikuphatikizapo nkhani za ophunizira, nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunizira komanso amene adzakhale ma cheyamani kuchokera pa abale amene bungwe la akulu linasankha. Aliyense amene wapatsidwa nkhani za ophunzira ayenera kudziwitsidwa kutatsala milungu yosachepera itatu kuti akambe nkhaniyo, pogwiritsa ntchito fomu ya Nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (S-89). M’bale amene amayang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ayenera kuonesetsa kuti ndandanda ya misonkhano yonse yaikidwa pa bolodi la mpingo. Bungwe la akulu lingasankhe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti azimuthandiza. Komabe akulu okha ndi amene ayenera kugawa nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunzira.

TCHEYAMANI WA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  22. Mlungu uliwonse, mkulu azipemphedwa kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. (Mipingo yomwe ili ndi akulu ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapemphedwe kukhala tcheyamani, ngati pakufunika kutero.) Tcheyamani azikamba mawu oyamba ndi omaliza, ndipo ndi amenenso ali ndi udindo wotsogolera poikambirana mavidiyo a zitsanzo za ulaliki. Aziitananso okamba nkhani zosiyanasiyana za msonkhanowu ndipo ngati akulu ndi ochepa, akhoza kumakambanso nkhani zina. Tcheyamani azilankhula mwachidule kwambiri nkhani iliyonse ikatha komanso akamaitana wokamba nkhani yotsatira. Bungwe la akulu liyenera kusankha akulu oyenerera kuti azikhala matcheyamani ndipo azisinthanasinthana. Malinga ndi mmene zilili pa mpingopo, mwina woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu angamakhale tcheyamani mobwerezabwereza kusiyana ndi akulu ena. Mkulu amene anavomerezedwa kuti azichititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo ndiye kuti ndi woyeneranso kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. Mkulu amene wasankhidwa kukhala tcheyamani ayenera kupereka malangizo achikondi komanso kuyamikira abale ndi alongo amene akamba nkhani za ophunzira. Tcheyamani ayenera kuonetsetsanso kuti misonkhano ikutha pa nthawi yake. (Onani  ndime 14 ndi  17.) Ngati tcheyamani angakonde komanso ngati kupulatifomu kuli malo okwanira, iye akhoza kuima pa maikofoni ena pambali kuti azilankhulirapo, amene akukamba nkhani yotsatira atafika kale pamaikofoni ake. Akhoza kusankhanso zokhaliratu kupulatifomuko pampando ataikanso tebulo lake kuti aziitana amene akukamba nkhani za ophunzira ndiponso kuwapatsa malangizo ali kupulatifomu komweko. Izi zingathandize kuti nthawi isawonongeke.

MLANGIZI WOTHANDIZA

   23. Ngati n’zotheka, sankhani mkulu amene amakamba bwino nkhani kuti akhale mlangizi wothandiza. Mlangiziyu azipereka malangizo kwa akulu ndi atumiki othandiza amene akamba nkhani zosiyanasiyana pamisonkhano yonse yampingo kaya ndi Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, nkhani ya onse, Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo. (Onani ndime 17.) Ngati mumpingomo muli akulu ambiri amene amakamba bwino nkhani, mungamasinthe mlangizi wothandiza chaka chilichonse. N’zosafunika kuti mlangizi wothandiza azipereka malangizo pamapeto a nkhani iliyonse.

MAKALASI ENA

 24. Mipingo ingakhale ndi makalasi angapo mogwirizana ndi kuchuluka kwa ophunzira. Kalasi iliyonse ikhale ndi woyang’anira woyenerera ndipo ngati n’kotheka akhale mkulu. Mtumiki wothandiza woyenerera angagwiritsidwenso ntchito kukalasi B ngati zili zoyenera kutero. Bungwe la akulu liyenera kusankha m’bale kapena abale amene angakhale pa udindo umenewu, komanso ngati zili zofunika kuti abalewo azisinthanasinthana. Mlangiziyo ayenera kutsatira malangizo amene ali mu  ndime 16. Anthu ayenera kupemphedwa kuti apite kukalasi B pambuyo pa mbali yakuti Mfundo Zothandiza m’chigawo cha Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu. Iwo ayenera kubwerera chigawo cha Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki chikatha. Pakakhala mavidiyo a zitsanzo za ulaliki, abale ndi alongo amene ali kukalasi B ayenera kuonerera ndi kukambirana mavidiyowo kukalasi B komweko, ngati zili zotheka kutero. Mwina m’bale amene akutsogolera kalasi B angaonetse mavidiyowo pakompyuta kapena pachipangizo china cha m’manja.

MAVIDIYO

 25. Pamsonkhanowu tizionera mavidiyo amene asankhidwa. Mavidiyo amene tizionera pamsonkhanowu azipezeka pa pulogalamu ya JW Library® ndipo azitheka kuwatsegula pa zipangizo zosiyanasiyana. Nthawi zina, mavidiyo monga a zitsanzo za ulaliki tizingawaonerenso pamsonkhano wokonzekera utumiki wakumunda, ngati anaonetsedwa kale pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.