Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 39-43

Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake

Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake

Zedekiya sanamvere zimene Yehova anamuuza zoti akadzipereke yekha kwa mfumu ya Babulo

39:4-7

  • Ana a Zedekiya anaphedwa iye akuona ndipo kenako anamukolowola maso, anamumanga ndi maunyolo amkuwa n’kukamuika m’ndende ku Babulo mpaka anafera komweko

Ebedi-meleki anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova komanso ankadera nkhawa Yeremiya

39:15-18

  • Yehova analonjeza kuti adzapulumutsa Ebedi-meleki pamene Yuda azidzawonongedwa

Yeremiya analalikira molimba mtima kwa zaka zambiri Yerusalemu asanawonongedwe

40:1-6

  • Yehova anateteza Yeremiya pamene mzinda wa Yerusalemu unazunguliridwa ndi adani ndipo anachititsa kuti Ababulo amumasule