Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kusamalira Malo Athu Olambirira

Kusamalira Malo Athu Olambirira

Nyumba zathu za Ufumu si nyumba wamba, koma ndi malo amene timalambirirako Yehova. Ndiye kodi aliyense angatani kuti azigwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu? Onerani vidiyo yakuti Kusamalira Malo Athu Olambirira, ndipo kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi m’Nyumba ya Ufumu mumachitika zotani?

  2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukonza Nyumba ya Ufumu kuti izikhala yaukhondo komanso yooneka bwino?

  3. Kodi ndi ndani amene ayenera kukonza Nyumba ya Ufumu?

  4. Kodi kupewa ngozi n’kofunika bwanji, nanga m’vidiyoyi taona zitsanzo ziti zimene zingatithandize kupewa ngozi?

  5. Kodi tingalemekeze bwanji Yehova ndi ndalama zimene timapereka?

KODI INEYO NDINGATHANDIZE NAWO BWANJI?