Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

May 1-7

YEREMIYA 32-34

May 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Chizindikiro Chosonyeza Kuti Aisiraeli Adzabwerera Kwawo”: (10 min.)

  • Yer. 32:6-9,15—Yehova anauza Yeremiya kuti agule munda ngati chizindikiro choti Aisiraeli adzabwerera kwawo (it-1 105 ¶2)

  • Yer. 32:10-12—Pamene Yeremiya ankagula munda, anatsatira malamulo onse ofunika (w07 3/15 11 ¶3)

  • Yer. 33:7,8—Yehova analonjeza kuti ‘adzayeretsa’ anthu ake omwe anali ku ukapolo (jr 152 ¶22-23)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yer. 33:15—Kodi “mphukira” ya Davide ndi ndani? (jr 173 ¶10)

  • Yer. 33:23, 24—Kodi “mabanja awiri” amene akunenedwa palembali ndi ati? (w07 3/15 11 ¶4)

  • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 32:1-12

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani onse kuti azigwiritsa ntchito vidiyo yothandiza pogawira kabuku kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 6

 • Zofunika Pampingo: (15 min.) Mukhoza kukambirana mfundo zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka. (yb16 67-71)

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 23 ¶1-14

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero