Akukonza Nyumba ya Ufumu ku Switzerland

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU May 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki za Nsanja ya Olonda komanso kuphunzitsa choonadi chokhudza zimene zili mtsogolo. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Chizindikiro Chosonyeza Kuti Aisiraeli Adzabwerera Kwawo

Kodi Yehova anamulonjeza chiyani mneneri Yeremiya pa nthawi imene anamuuza kuti akagule munda? Kodi Yehova anasonyeza bwanji ubwino wake?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Ebedi-meleki Ndi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani ya Kulimba Mtima Komanso Kukoma Mtima

Ebedi-meleki anachita zinthu molimba mtima komanso mosazengereza pokauza Mfumu Zedekiya zomwe zinachitikira Yeremiya komanso anakomera mtima mneneri wa Mulungu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kusamalira Malo Athu Olambirira

Popeza malo athu olambirira amadziwika ndi dzina loyera la Mulungu, n’kofunika kumawasamalira komanso kumawakonza akawonongeka. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake

Mneneri Yeremiya komanso Mfumu Zedekiya amatchulidwa mu nkhani zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu koma anthuwa anali osiyana kwambiri.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova Sangaiwale Chikondi Chanu

Kodi Yehova amawaona bwanji atumiki ake okalamba omwe sangathe kuchita zambiri pomutumikira?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Leka ‘Kufunafuna Zinthu Zazikulu’

Baruki ankalambira Yehova komanso ankathandiza Yeremiya mokhulupirika, koma nthawi ina anachita zinthu mosaganiza bwino. Kodi ankafunika kuchita chiyani kuti adzapulumuke pamene Yerusalemu ankawonongedwa?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Amadalitsa Anthu Odzichepetsa Ndipo Amalanga Odzikuza

Ababulo odzikuza ankachitira nkhanza anthu a Yehova. Aisiraeli omwe analapa anamasulidwa mu ukapolo, koma kodi n’chiyani chinachitikira Babulo?