Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

NSANJA YA OLONDA

Funso: Kodi inuyo mumaona kuti mawu awa adzakwaniritsidwadi?

Lemba: Chiv. 21:3, 4

Perekani Magaziniyo: Magazini iyi ikufotokoza mmene Mulungu adzakwaniritsire mawu amenewa komanso mmene moyo udzakhalire mawuwa akadzakwaniritsidwa.

NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)

Funso: Taonani funso ili. [Musonyezeni funso loyamba patsamba 16 komanso zimene anthu ena amayankha.] Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Lemba: Sal. 83:18

Perekani Magaziniyo: Nkhaniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza dzina la Mulungu.

BAIBULO LIMAPHUNZITSA CHIYANI

Funso: Anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli. Koma kodi mukudziwa kuti zimenezi n’zosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?

Lemba: 1 Yoh. 5:19

Perekani Bukulo: Bukuli likufotokoza momveka bwino zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi zinanso zambiri.

LEMBANI NJIRA INA IMENE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.