Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 1-10

Tizilemekeza Yesu Kuti Tikhale Pamtendere ndi Yehova

Tizilemekeza Yesu Kuti Tikhale Pamtendere ndi Yehova

Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakana kukhulupirira Yehova ndi Yesu

2:1-3

  • Baibulo linaneneratu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana sadzamvera ulamuliro wa Yesu koma adzakhazikitsa maulamuliro awo

  • Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba pa nthawi yomwe Yesu anali padzikoli ndipo ukukwaniritsidwa kwambiri masiku ano

  • Wamasalimo ananena kuti anthu amang’ung’udza za zinthu zopanda pake, kutanthauza kuti zolinga zawo n’zopanda phindu ndipo sizingakwaniritsidwe ngakhale pang’ono

Amene amalemekeza Mfumu imene Yehova anasankha adzapeza moyo

2:8-12

  • Anthu onse omwe amatsutsa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu adzawonongedwa

  • Aliyense amene amalemekeza Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu akhoza kupeza mtendere ndiponso adzapulumuka