Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 25

“Khalanibe Maso”

“Khalanibe Maso”

25:1-12

Ngakhale kuti fanizo la anamwali 10 limanena za otsatira odzozedwa a Khristu, mfundo zake zimakhudza Akhristu onse. (w15 3/15 12-16) Iye anati, “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi mungakwanitse kufotokoza bwinobwino fanizoli?

  • Mkwati (vesi 1)​—Yesu

  • Anamwali ochenjera omwe anakonzekera (vesi 2)​—Akhristu odzozedwa omwe ndi okonzeka kugwira ntchito yawo mokhulupirika ndipo adzawala ngati zounikira mpaka m’nthawi yamapeto. (Afil. 2:15)

  • Mawu ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)​—Chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu

  • Anamwali opusa (vesi 8)​—Akhristu odzozedwa omwe anapita kukachingamira mkwati koma analephera kukhalabe maso ndipo analephera kukhalabe okhulupirika

  • Anamwali ochenjera anakana kugawana mafuta awo ndi anamwali opusa (vesi 9)​—Pambuyo poti Yehova wadinda chidindo chomaliza Akhristu odzozedwa, zidzakhala zosatheka kuti odzozedwa okhulupirikawa athandize osakhulupirika aja

  • “Mkwati anafika” (vesi 10)​—Yesu adzabwera kudzapereka chiweruzo chakumapeto kwa chisautso chachikulu

  • Anamwali ochenjera analowa limodzi ndi mkwati m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa (vesi 10)​—Yesu adzasonkhanitsa odzozedwa okhulupirika n’kupita nawo kumwamba, koma osakhulupirika sadzalandira nawo mphoto imeneyi