Akuitanira anthu ku Chikumbutso ku Slovenia

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU March 2018

Zimene Tinganene

Kukambirana pogwiritsa ntchito kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso komanso mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani Yesu anafa? Kodi dipo la Yesu lingatithandize bwanji?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenera Kukhala Mtumiki Wanu”

Kodi timakonda kuchita utumiki umene ungachititse kuti ena aziona kuti ndife ofunika kwambiri komanso azitilemekeza? Munthu wodzichepetsa amagwira ntchito zimene ndi Yehova Mulungu yekha angamuone.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzitsatira Malamulo Awiri Aakulu Kwambiri

Kodi Yesu ananena zotani zokhudza malamulo awiri aakulu kwambiri m’Baibulo? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timatsatira malamulo amenewa?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu Komanso Anzathu?

Tiyenera kumakonda Mulungu komanso anzathu. Njira imodzi imene tingakulitsire chikondi chimenechi ndi kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Pitirizani Kukhala Maso M’masiku Otsiriza Ano

Anthu ambiri masiku ano amalola kuti zinthu zatsiku ndi tsiku ziwalepheretse kuchita zinthu zokhudza kulambira Kodi Akhristu olimba mwauzimu amasiyana bwanji ndi anthu a m’dzikoli?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mapeto a Dziko Loipali Ali Pafupi Kwambiri

Kodi mawu a Yesu akusonyeza bwanji kuti tikukhala m’nthawi yamapeto yeniyeni? Funso limeneli likuyankhidwa mu vidiyo yakuti Mapeto a Dziko Loipali Ali Pafupi Kwambiri.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Khalanibe Maso”

M’fanizo la anamwali 10, kodi ndi ndani amene ali mkwati, anamwali ochenjera komanso anamwali opusa? Nanga kodi fanizo limeneli likukukhudzani bwanji?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera

Phunziro likangoyamba kumene, tizithandiza munthu kuti akhale ndi chizolowezi choti azikonzekera phunzirolo. Kodi tingachite bwanji zimenezi?