Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 34-37

Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino

Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino

“Usapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa”

37:1, 2

  • Musasiye kutumikira Yehova poona kuti anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino. M’malo mwake, muziganizira zimene mungachite potumikira Yehova komanso madalitso amene Iye adzakupatseni

“Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino”

37:3

  • Muzikhulupirira kuti Yehova angakuthandizeni kuthana ndi mavuto ndiponso nkhawa zanu. Komanso angakuthandizeni kukhalabe okhulupirika

  • Muzigwira mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu

“Sangalala mwa Yehova”

37:4

  • Muzikhala ndi nthawi yowerenga Baibulo ndiponso kusinkhasinkha n’cholinga choti mumudziwe bwino Yehova

“Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako”

37:5, 6

  • Muzikhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova angakuthandizeni kuthana ndi vuto lina lililonse

  • Muzisonyezabe khalidwe labwino anthu akamakutsutsani, kukuzunzani komanso kukunenerani zinthu zabodza

“Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse”

37:7-9

  • Muzipewa kuchita zinthu mopupuluma chifukwa zingachititse kuti musamasangalale komanso zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova

“Ofatsa adzalandira dziko lapansi”

37:10, 11

  • Yesetsani kukhala ofatsa ndi kuyembekezera Yehova modzichepetsa kuti adzachotse zosalungama zonse zomwe zikukuchitikirani

  • Muzithandiza Akhristu anzanu komanso kulimbikitsa amene ali ndi nkhawa powakumbutsa kuti dziko latsopano lili pafupi kwambiri

Ufumu wa Mesiya udzabweretsa madalitso osaneneka