Ofalitsa akulalikira pogwiritsa ntchito kapepala ku Malta

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU June 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Mfundo zokuthandizani pogawira Galamukani! ndi timapepala. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino

Muzigwiritsa ntchito malangizo othandiza a mu Salimo 37.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa

N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mavidiyowa mu utumiki? Nanga angatithandize bwanji kuwonjezera luso lophunzitsa?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Amasamalira Anthu Omwe Akudwala

Mawu a Davide opezeka mu Salimo 41 akhoza kulimbikitsa atumiki okhulupirika amene akudwala kapenanso amene akukumana ndi mavuto enaake?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Sadzasiya Anthu Amtima Wosweka

Mu Salimo 51, Davide akufotokoza mmene tchimo lake linamukhudzira. N’chiyani chinamuthandiza kuti alape?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ufumu wa Mulungu Wakwanitsa Zaka 100 Ndipo Ukulamulirabe

Gwiritsani ntchito mafunso pokambirana zomwe Ufumu wa Mulungu wakwanitsa kuyambira 1914.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Umutulire Yehova Nkhawa Zako”

Mawu amene Davide analemba pa Salimo 55:22 angatithandize tikakumana ndi vuto lina lililonse.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Mulungu Ndiye Mthandizi Wanga”

Davide anatamanda Yehova chifukwa cha Mawu ake. Kodi ndi mavesi ati amene anakuthandizani mutakumana ndi mavuto?