Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 60-68

Tamandani Yehova Wakumva Pemphero

Tamandani Yehova Wakumva Pemphero

Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukwaniritsa zomwe munamulonjeza

61:1, 8

  • Tikamauza Yehova m’pemphero zimene tamulonjeza, zimatithandiza kuti tikwaniritsedi zimene tamulonjezazo

  • Chinthu chofunika kwambiri chimene tingalonjeze Mulungu n’choti tidzamutumikira kwa moyo wathu wonse

Hana

Muzisonyeza kuti mumakhulupirira Yehova pomuuza zakukhosi kwanu

62:8

  • Mapemphero athu angakhale abwino kwambiri ngati titamafotokozera Yehova zimene zili mumtima mwathu

  • Tikamatchula m’pemphero chinthu chenicheni chimene tikufuna, sitivutika kuzindikira kuti Yehova wayankha mapemphero athu

Yesu

Yehova amamva mapemphero a anthu a mitima yabwino

65:1, 2

  • Yehova amamvetsera mapemphero a “anthu a mitundu yonse” omwe amafunitsitsa kumudziwa komanso kuchita zofuna zake

  • Tikhoza kupemphera kwa Yehova nthawi iliyonse

Koneliyo

Lembani nkhani zina zimene mukufuna kutchula m’mapemphero anu.