Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ndandanda ya Upainiya Wokhazikika

Ndandanda ya Upainiya Wokhazikika

Kuti munthu akwanitse kuchita upainiya wokhazikika amafunika kugawa bwino nthawi yake. Ngati mutamalalikira maola 18 pa mlungu, ndiye kuti mukhoza kupeza nthawi ina yochita zinthu zina komanso kupuma. Kuwonjezera pamenepa, simungavutike kukwanitsa maola ngati mutadwala mwadzidzidzi kapena ngati nyengo sili bwino. Ndandanda imene ili m’munsiyi ingakuthandizeni kugawa bwino nthawi yanu ngati mumagwira ntchito yaganyu, ntchito yolembedwa kapena ngati mumadwaladwala. Komanso ngati mutasintha zina ndi zina m’banja lanu, munthu mmodzi kapena angapo akhoza kuyamba upainiya mwezi wa September. Bwanji osakambirana zimenezi pa kulambira kwanu kwa pabanja kwa mlungu wotsatira?

NDIMAGWIRA NTCHITO YAGANYU

Lolemba

NTCHITO

Lachiwiri

NTCHITO

Lachitatu

NTCHITO

Lachinayi

Maola 6

Lachisanu

Maola 6

Loweruka

Maola 4

Lamlungu

Maola 2

NDIMAGWIRA NTCHITO YOLEMBEDWA

Lolemba

Maola Awiri

Lachiwiri

Maola Awiri

Lachitatu

MISONKHANO YA MKATI MWA MLUNGU

Lachinayi

Maola Awiri

Lachisanu

Maola Awiri

Loweruka

Maola 6

Lamlungu

Maola 4

NDIMADWALADWALA

Lolemba

KUPUMA

Lachiwiri

Maola 3

Lachitatu

Maola 3

Lachinayi

Maola 3

Lachisanu

Maola 3

Loweruka

Maola 3

Lamlungu

Maola 3