Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 79-86

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu ndi Ndani?

Kodi Munthu Wofunika Kwambiri pa Moyo Wanu ndi Ndani?

Munthu amene analemba Salimo 83 ayenera kuti anali mdzukulu wa Asafu, yemwe anakhalapo pa nthawi imene Mfumu Davide anali ndi moyo. Salimo limeneli linalembedwa pa nthawi imene atumiki a Yehova ankaopsezedwa ndi mitundu ina.

83:1-5, 16

  • Amene analemba Salimo limeneli anatchula kwambiri za dzina la Mulungu komanso ulamuliro wake m’malo moganizira kwambiri za moyo wake womwe unali pangozi

  • Masiku anonso atumiki a Mulungufe timaopsezedwa ndi anthu ena. Koma tikamakhalabe okhulupirika, dzina la Yehova limalemekezedwa

83:18

  • Yehova amafuna kuti tidziwe dzina lake

  • Zochita zathu ziyenera kumasonyeza kuti timaona Yehova kukhala wofunika kwambiri pa moyo wathu