Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 4-5

Zimene Tikuphunzira pa Zomwe Yesu Anaphunzitsa pa Ulaliki Wapaphiri

Zimene Tikuphunzira pa Zomwe Yesu Anaphunzitsa pa Ulaliki Wapaphiri

5:3

Kodi mumazindikira zosowa zanu zauzimu?

Mawu akuti “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” kwenikweni amatanthauza “anthu amene amapempha mzimu.” (Mat. 5:3) Tingasonyeze kuti tikufuna kuti Mulungu azititsogolera ndi mzimu wake ngati . . .

  • timawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku

  • timakonzekera komanso kupezeka pamisonkhano

  • timawerenga mabuku athu, komanso ngati n’zotheka, zinthu zosiyanasiyana zopezeka pawebusaiti yathu

  • timaonera pulogalamu ya JW Broadcasting ya mwezi uliwonse

Kodi ndingatani kuti nthawi zonse ndizikonda kuphunzira Mawu a Mulungu?