Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa

Tisamaiwale Kupempherera Akhristu Amene Akuzunzidwa

Baibulo linaneneratu kuti Satana adzatizunza n’cholinga choti asokoneze utumiki wathu. (Yoh. 15:20; Chiv. 12:17) Kodi tingathandize bwanji Akhristu anzathu amene akuzunzidwa m’mayiko ena? Tikhoza kumawapempherera. Paja “pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—Yak. 5:16.

Kodi tinganene chiyani m’mapemphero athu? Tikhoza kupempha Yehova kuti athandize abale ndi alongo athu kuti akhale olimba mtima. (Yes. 41:10-13) Tikhozanso kupemphera kuti akuluakulu a boma asachite chilichonse chosokoneza ntchito yathu yolalikira n’cholinga choti “tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere.”—1 Tim. 2:1, 2.

Pa nthawi imene Paulo ndi Petulo ankazunzidwa, Akhristu anzawo ankawatchula mayina powapempherera. (Mac. 12:5; Aroma 15:30, 31) Ngakhale kuti sitikudziwa mayina a anthu onse amene akuzunzidwa, tikhoza kutchula mpingo wawo, dziko lawo kapena dera lawo powapempherera.

Lembani madera amene kuli Akhristu amene akuzunzidwa omwe mukufuna kumawapempherera