Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

February 6-12

YESAYA 47-51

February 6-12
 • Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero

 • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

 • Kumvera Yehova Kumabweretsa Madalitso”: (10 min.)

  • Yes. 48:17—Kuti tizilambira Mulungu movomerezeka, tiyenera kutsatira malangizo ake (ip-2 131 ¶18)

  • Yes. 48:18—Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala (ip-2 131 ¶19)

  • Yes. 48:19—Kumvera Yehova kumabweretsa madalitso osatha (ip-2 132 ¶20-21)

 • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

  • Yes. 49:6—N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mesiya ndi “kuwala kwa mitundu ya anthu” ngakhale kuti ankalalikira Aisiraeli okha? (w07 1/15 9 ¶9)

  • Yes. 50:1—N’chifukwa chiyani Yehova anafunsa Aisiraeli kuti, kodi “chili kuti chikalata chothetsera ukwati wa mayi wanu?” (ip-2 152 ¶2; it-1-E 643 ¶4-5)

  • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

 • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yes. 51:12-23

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

 • Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Dziwani izi: Palibe vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki wa kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? Choncho pemphani ofalitsa awiri kuti achite chitsanzo cha mmene tingagawirire kabukuka. M’mwezi wa February, ofalitsa angagawire kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? (Onaninso bokosi lakuti Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

 • Nyimbo Na. 89

 • Zofunika Pampingo: (7 min.) Mukhoza kukambirana zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka. (yb16 144-145)

 • Khalani Bwenzi la Yehova—Muzimvera Yehova: (8 min.) Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo yakuti Khalani Bwenzi la YehovaMuzimvera Yehova. Kenako kambiranani mafunso awa: Kodi chifukwa chachikulu chimene tiyenera kumvera Yehova ndi chiti? (Miy. 27:11) Kodi ana ayenera kumvera Yehova pa zinthu ziti? Nanga akuluakulu ayenera kumvera Yehova pa zinthu ziti?

 • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 17 ¶1-13

 • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

 • Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero