Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 52-57

Khristu Anavutika Chifukwa cha Ife

Khristu Anavutika Chifukwa cha Ife

“Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa. . . . Ifeyo tinamuona ngati wosautsidwa, wokwapulidwa ndi Mulungu, ndiponso wozunzidwa”

53:3-5

  • Yesu ankanyozedwa ndiponso kunamiziridwa kuti ndi wonyoza Mulungu. Anthu ena ankakhulupirira kuti Mulungu ndi amene ankamusautsa kapena kuti kumulanga

“Zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe . . . ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda Yehova.”

53:10

  • N’zosachita kufunsa kuti Yehova anavutika kwambiri ataona mwana wake akuphedwa. Komabe anasangalala chifukwa chakuti Yesu sanasiye kukhala wokhulupirika. Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa ndipo izi zinathandiza kutsutsa zimene Satana ananena zoti atumiki a Mulungu sangakhale okhulupirika atakumana ndi mavuto. Zinachititsanso kuti anthu olapa apeze madalitso. Choncho imfa yakeyi inathandiza kukwaniritsa zimene Yehova ankafuna