Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 9-11

Anthu Okhulupirika Amatsatira Malangizo a Gulu la Yehova

Anthu Okhulupirika Amatsatira Malangizo a Gulu la Yehova

Anthu okhulupirika anatsatira malangizo osiyanasiyana a gulu la Yehova

10:28-30, 32-39; 11:1, 2

  • Anthu a Yehova anakonzekera Chikondwerero cha Misasa ndipo anachita motsatira malangizo

  • Tsiku lililonse anthu ankasonkhana kuti amvetsere Chilamulo cha Mulungu ndipo ankasangalala

  • Anthu anaulula machimo, anapemphera komanso anapempha Yehova kuti awadalitse

  • Anthu anavomereza kuti apitiriza kutsatira malangizo ochokera kwa Yehova

• Anatsatira malangizo a gulu la Yehova pochita zinthu izi:

  • Ankakwatirana ndi anthu okhawo amene ankalambira Yehova

  • Ankapereka ndalama zothandizira pa kulambira koona

  • Ankasunga Sabata

  • Ankapereka nkhuni zomwe ankazigwiritsa ntchito paguwa lansembe

  • Ankapereka kwa Yehova mbewu zoyamba kucha ndiponso ziweto zoyamba kubadwa