Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 6-10

Mesiya Anakwaniritsa Ulosi

Mesiya Anakwaniritsa Ulosi
ONANI

Kudakali zaka zambiri kuti Yesu abadwe, Yesaya ananeneratu kuti Mesiya adzalalikira “m’chigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.” Yesu anakwaniritsa ulosi umenewu chifukwa analalikira uthenga wabwino m’chigawo chonse cha Galileya.—Yes. 9:1, 2.

  • Anachita chozizwitsa chake choyamba pa ukwati winawake—Yoh. 2:1-11 (ku Kana)

  • Anasankha atumwi ake—Maliko 3:13, 14 (kufupi ndi ku Kaperenao)

  • Analalikira ulaliki wake wa paphiri—Mat. 5:1–7:27 (pafupi ndi ku Kaperenao)

  • Anaukitsa mwana yekhayo wa mkazi wina wamasiye—Luka 7:11-17 (ku Naini)

  • Anaonekera kwa ophunzira ake oposa 500 pambuyo poti waukitsidwa—1 Akor. 15:6 (ku Galileya)