Kuchititsa phunziro la Baibulo ku Chile

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU December 2016

Zitsanzo za Ulaliki

Mfundo zokuthandizani pogawira Galamukani!, ndiponso zomwe tingachite pophunzitsa anthu chifukwa chake anthu akukumana ndi mavuto. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Tiyeni Tipite Kukakwera Phiri la Yehova”

Mneneri Yesaya anafotokoza za zida zankhondo zimene zidzasinthidwe kukhala zipangizo zolimira. Zimene ananenazi zikusonyeza kuti anthu a Yehova azidzakhala mwa mtendere. (Yesaya 2:4)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizifika Anthu Pamtima ndi Buku Lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?

Buku la ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’ limathandiza amene akuphunzira Baibulo kudziwa mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mesiya Anakwaniritsa Ulosi

Mneneri Yesaya ananeneratu kuti Mesiya adzalalikira m’chigawo cha Galileya. Yesu anakwaniritsa ulosi umenewu pamene ankalalikira uthenga wabwino.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

Kodi tingatsanzire bwanji Yesaya pa nkhani ya kukhala ndi mtima wodzipereka komanso chikhulupiriro? Onerani vidiyo kuti mudziwe za banja lomwe linasamukira kudera limene kukufunika olalikira ambiri.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Dziko Lapansi Lidzadzaza ndi Anthu Odziwa Yehova

Kodi ulosi wa Yesaya wonena za paradaiso padziko lapansi unakwaniritsidwa bwanji m’nthawi? Kodi ukukwaniritsidwa bwanji panopa? Nanga udzakwaniritsidwa bwanji mtsogolo?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zimene Mulungu Amatiphunzitsa Zimatithandiza Kuti Tisakhale Atsankho

Anthu awiri amene kale ankadana anayamba kugwirizana kwambiri—zimenezi zinatheka chifukwa cha zimene Mulungu amatiphunzitsa.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Munthu Akamagwiritsa Ntchito Udindo Wake Molakwika Amachotsedwa pa Udindowo

Kodi Sebina ankayenera kuchita chiyani pa udindo wake? N’chifukwa chiyani Yehova anam’chotsa pa udindowo n’kuikapo Eliyakimu?