Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Chikhulupiriro

Muzikhala ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo​—Chikhulupiriro

N’CHIFUKWA CHIYANI KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO N’KOFUNIKA?

  • Chikhulupiriro n’chofunika kuti tizichita zimene Mulungu amasangalala nazo.​—Aheb. 11:6

  • Kukhulupirira zimene Mulungu anatilonjeza kumatithandiza kupirira tikakumana ndi mayesero.​—1 Pet. 1:6, 7

  • Kupanda chikhulupiriro kungachititse munthu kuti achite tchimo.​—Aheb. 3:12, 13

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TILI NDI CHIKHULUPIRIRO?

Kodi ndingalimbitse bwanji chikhulupiriro changa komanso cha anthu a m’banja langa?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA ZINTHU ZIMENE ZINGAKULIMBIKITSENI KUKHALA OKHULUPIRIKA​—CHIKHULUPIRIRO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi “chikhulupiriro chopanda chinyengo” chimakhala chotani? (1 Tim. 1:5)

  • Kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, kodi tiyenera kupewa maganizo olakwika ati?

  • N’chifukwa chiyani tidzafunika kukhala ndi chikhulupiriro pa nthawi ya chisautso chachikulu? (Aheb. 10:39)