Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizithandiza Ophunzira Baibulo Athu Kuti Adzipereke Komanso Kubatizidwa

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizithandiza Ophunzira Baibulo Athu Kuti Adzipereke Komanso Kubatizidwa

N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA? Anthu amene akuphunzira Baibulo ayenera kudzipereka komanso kubatizidwa ngati akufuna kuti Yehova aziwakonda. (1 Pet. 3:21) Ndipo munthu amakhala wotetezeka mwauzimu akabatizidwa n’kumachita zimene analonjeza Yehova pamene ankadzipereka. (Sal. 91:1, 2) Mkhristu amadzipereka kwa Yehova osati kwa munthu, ntchito kapena bungwe linalake. Choncho kuti tithandize munthu kuti adzipereke ndi kubatizidwa, choyamba tiyenera kumuthandiza kuti azikonda kwambiri Yehova.—Aroma 14:7, 8.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Mukamaphunzira ndi munthuyo, muzikambirana mfundo zomwe zingamuthandize kudziwa bwino Yehova. Mulimbikitseni kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kuti azipemphera kwa Yehova “mosalekeza.”—1 Ates. 5:17; Yak. 4:8

  • Mulimbikitseni kuti akhale ndi cholinga choti azadzipereke kwa Yehova kenako n’kubatizidwa. Muthandizeninso kukwaniritsa zolinga zing’onozing’ono, monga kuyankha pamisonkhano kapena kulalikira kwa anthu oyandikana nawo nyumba kapenanso kwa anzake a kuntchito. Kumbukirani kuti Yehova sakakamiza munthu kuti azimutumikira. Choncho, munthu ayenera kusankha yekha kuti azimutumikira.—Deut. 30:19, 20

  • Mulimbikitseni wophunzira wanuyo kuti ayesetse kusintha makhalidwe ake n’cholinga choti azikondweretsa Yehova komanso kuti adzabatizidwe. (Miy. 27:11) Popeza makhalidwe ena amakhala ovuta kuwasiya, mufunika kupitirizabe kuthandiza wophunzira wanuyo kuti avule umunthu wake wakale n’kuvala watsopano. (Aef. 4:22-24) Mungachitenso bwino kumakambirana naye nkhani za mu Nsanja ya Olonda za mutu wakuti, “Baibulo Limasintha Anthu”

  • Mufotokozereni madalitso amene mwapeza chifukwa chotumikira Yehova.—Yes. 48:17, 18