Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 87-91

Pitirizani Kukhala M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba

Pitirizani Kukhala M’malo Otetezeka a Wam’mwambamwamba

Timatetezeka mwauzimu tikakhala “m’malo achitetezo” a Yehova

91:1, 2, 9-14

  • Kuti tikhale m’malo achitetezo a Yehova, timafunika kudzipereka komanso kubatizidwa

  • Anthu amene sakhulupirira Mulungu sadziwa malo amenewa

  • Anthu amene ali m’malo achitetezo a Yehova sakopeka ndi anthu kapena chilichonse chimene chingapangitse kuti asiye kukhulupirira komanso kukonda Mulungu

“Wosaka mbalame” akufunitsitsa kutigwira

91:3

  • Mbalame ndi zochenjera kwambiri, ndipo ndi zovuta kugwira

  • Wosaka mbalame amayang’anitsitsa zimene mbalamezo zimakonda, ndipo amakonza misampha kuti azigwire

  • Nayenso Satana, yemwe ndi “wosaka mbalame,” amayang’anitsitsa zimene atumiki a Yehova amakonda kuchita ndipo amatchera misampha n’cholinga choti awagwire

Misampha 4 yoopsa imene Satana amagwiritsa ntchito kuti atikole:

  • Kuopa Anthu

  • Kukonda Chuma

  • Zosangalatsa Zosayenera

  • Kusemphana Maganizo ndi Anthu Ena