Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 17-21

Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu

Muzilola Kuti Yehova Aziumba Maganizo ndi Makhalidwe Anu

Muzivomereza ndi mtima wonse kuti Yehova akuumbeni

18:1-11

  • Yehova amatiumba pogwiritsa ntchito malangizo kapena uphungu

  • Tiyenera kukhala oumbika komanso omvera

  • Yehova satikakamiza kuchita zinthu zimene sitikufuna

Woumba amatha kuchita zimene akufuna ndi chinthu chimene akuumbacho

  • Popeza Yehova anatipatsa ufulu wosankha zochita, tingasankhe kuvomereza kuti azitiumba kapena kukana

  • Yehova amachita zinthu ndi anthu mogwirizana ndi mmene anthuwo akutsatirira malangizo ake

Kodi ndikufuna kuti Yehova andiumbe m’njira ziti?