Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 22-24

Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?

Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?

Yehova anayerekezera anthu ndi nkhuyu

24:5

  • Ayuda okhulupirika omwe anali ku Babulo anali ngati nkhuyu zabwino

24:8

  • Mfumu Zedekiya komanso Ayuda ena osakhulupirika amene ankachita zoipa anali ngati nkhuyu zoipa

Kodi tingatani kuti tikhale ndi “mtima wodziwa” Yehova?

24:7

  • Yehova angatipatse ‘mtima womudziwa’ ngati timaphunzira Mawu ake ndi kugwiritsa ntchito zimene timaphunzirazo

  • Tiyenera kudzifufuza moona mtima n’kusintha makhalidwe ndi zilakolako zoipa zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova

Dzifunseni kuti: Kodi ndili ndi “mtima wodziwa” Yehova? Nanga ndingatani kuti ndikhale nawo?