Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo

Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo

Chaka chilichonse timayembekezera mwachidwi phwando la chakudya chauzimu lomwe timasangalala nalo pamisonkhano yachigawo. Pofuna kuti anthu enanso adzalawe ubwino wa Yehova, tidzayesetsa kuitanira anthu ambiri kumsonkhano wachigawo. (Sal. 34:8) M’mipingo yonse, mabungwe a akulu adzasankha njira yabwino yomwe mpingo wawo ungatsatire pogawira timapepalati.

MFUNDO ZOFUNIKA KUZIKUMBUKIRA

  • Kodi msonkhano wathu udzachitika liti?

  • Kodi mpingo wathu udzayamba liti ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?

  • Kodi ndi masiku ati amene mpingo wathu uzidzachita misonkhano yokonzekera ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?

  • Kodi ndikufuna kudzakwaniritsa zolinga ziti pa ntchito yoitanira anthuyi?

  • Kodi ndi anthu ati omwe ndikufuna kudzawaitana?

ZIMENE MUNGANENE

Pambuyo popereka moni munganene kuti:

“Tikugwira ntchito yomwe ikuchitika padziko lonse yoitanira anthu kumsonkhano wofunika kwambiri. Pakapepalaka talembapo nthawi ndi malo omwe msonkhanowu udzachitikire. Tidzasangalala kwambiri kukhala nanu pamsonkhanowu.”

TIDZATHANDIZE ANTHU ACHIDWI

Ngakhale kuti tikufunitsitsa kudzaitanira anthu ambiri kumsonkhanowu, tikufunika kudzathandiza anthu omwe asonyeza chidwi kuti aphunzire zambiri.

Kumapeto kwa mlungu, tingadzagawire kapepalaka limodzi ndi magazini.