Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 28-32

Yobu Ndi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani ya Kukhala ndi Mtima Wosagawanika

Yobu Ndi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani ya Kukhala ndi Mtima Wosagawanika

Yobu ankatsatira mfundo za makhalidwe abwino za Yehova ndi mtima wonse

31:1

  • Iye ankakonda kwambiri mkazi wake ndipo sanalole kuti maso ake aziyang’ananitsitsa akazi ena mowalakalaka

Yobu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kukhala bwino ndi ena

31:13-15

  • Anali wodzichepetsa, wachilungamo ndiponso wachifundo. Ankakonda anthu onse, olemera ndi osauka omwe

Yobu anali woolowa manja ndiponso sanali wodzikonda

31:16-19

  • Ankathandiza anthu ovutika