Malangizo a Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
Zimene Zili M’malangizowa
Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu 24
1. Malangizo amene ali m’dokyumentiyi azithandiza aliyense amene ali ndi mbali pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Iwo akuyenera kumawerenga malangizo a mbali yawo amene ali mu kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu komanso malangizo a mmene angachitire mbaliyo kuchokera m’dokyumenti ino. Azichita zimenezi asanayambe kukonzekera. Ofalitsa onse azilimbikitsidwa kuti alembetse n’cholinga choti azipatsidwa nkhani za ophunzira. Anthu enanso amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse, ndipo amatsatira mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa komanso mfundo za Chikhristu pa moyo wawo, angalembetse kuti azipatsidwa nkhani za ophunzirazi. Woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu akuyenera kufotokozera aliyense amene si wofalitsa koma ali ndi chidwi cholembetsa nawo m’sukuluyi kuti adziwe zimene zimafunikira komanso aone ngati ali woyenerera kulembetsa nawo. Zimenezi zikuyenera kuchitika ali limodzi ndi munthu amene amachita naye phunziro la Baibulo (kapena makolo ake amene ndi a Mboni). Zimene munthu amafunikira kukwaniritsa kuti ayambe kutenga nawo mbali m’sukulu ya utumiki ndi zofanana ndi zimene zimafunikira kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa. —od mutu 8 ndime 8.
MAWU OYAMBA
2. 1 Miniti. Wiki iliyonse, pambuyo pa nyimbo komanso pemphero loyamba, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu azifotokoza mwachidule zimene tiphunzire. Tcheyamaniyo azitsindika kwambiri mfundo zimene abale ndi alongo angapindule nazo kwambiri.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
3. Nkhani: 10 minitsi. Mu kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu pazikhala mutu komanso mfundo zikuluzikulu ziwiri kapena zitatu. Nkhaniyi iyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Tikamayamba buku latsopano la m’Baibulo, tizionera vidiyo. Wokamba nkhaniyo angasonyeze kugwirizana pakati pa vidiyoyo ndi nkhani yake. Koma ayeneranso kuonetsetsa kuti wafotokoza mfundo zimene zili munkhani yake. Komanso ayenera kufotokozera zithunzi zimene zaikidwa zomwe zimakonzedwa kuti zithandize kumveketsa mfundo za munkhaniyo. Akhozanso kuwonjezera malifalensi ena amene akuthandiza kumveketsa bwino mfundo za munkhani yake.
4. Mfundo Zothandiza: 10 minitsi. Iyi ndi nkhani ya mafunso ndi mayankho yopanda mawu oyamba ndiponso omaliza. Nkhaniyi izikambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera. Iye ayenera kufunsa mafunso onse awiri. Komanso, akhoza kusankha kuwerenga mavesi onse amene aikidwa kapena ayi. Anthu amene alozedwa kuti ayankhe ayenera kufotokoza ndemanga zawo kwa nthawi yosapitirira masekondi 30.
5. Kuwerenga Baibulo: 4 Minitsi. Nkhaniyi iperekedwe kwa wophunzira wamwamuna. Ayenera kungowerenga mavesi amene wauzidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Tcheyamani ayenera kuthandiza munthuyo kuti amvetse zimene akuwerenga, awerenge molondola komanso mosadodoma, azisintha mawu, kupuma moyenera ndiponso kulankhula mwachibadwa. Popeza kuti mavesi ena amene abale azipatsidwa kuti awerenge azikhala ambiri ndipo ena azikhala ochepa, woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu ayenera kuganizira luso la wophunzira akamagawa nkhani zimenezi.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
6. 15 Minitsi. Chigawo chimenechi cha msonkhano chakonzedwa kuti chizithandiza aliyense kuti ayeserere zimene angachite mu utumiki komanso awonjezere luso lolalikira ndi kuphunzitsa. Ngati n’zotheka, akulu angapatsidwe nkhani za ophunzira. Wophunzira aliyense akuyenera kugwirirapo ntchito pa phunziro limene wapatsidwa kuti agwiritse ntchito kuchokera m’kabuku ka Kuphunzitsa kapena ka Muzikonda Anthu. Mbali imene mwapemphedwa kuti mugwiritsire ntchito imalembedwa monga lifalensi mu mkutira mawu omwe umaikidwa mu Kabuku ka Utumiki komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Nthawi zina muzikhala ndi nkhani yochita kukambirana ndi omvetsera. Nkhani imeneyi ikuyenera kuperekedwa kwa mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera.—Onani ndime 15 kuti mupeze zokhudza mmene mungachititsire mbali zokambirana ndi omvetsera.
7. Ulendo Woyamba: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wamkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, womuthandiza akhalenso wamkazi kapena munthu wa m’banja lake. Ngati yaperekedwa kwa wamwamuna, womuthandiza akhalenso wamwamuna kapena munthu wa m’banja lake. Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira. Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene mungakambe komanso mmene mungachitire mbaliyi, onani ndime 12 ndi 13.
8. Ulendo Wobwereza: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wa mkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, womuthandiza akhalenso wamkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, womuthandiza akhalenso wamwamuna. (km 5/97 tsa. 2) Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira. Wophunzira akuyenera kuonetsa zimene anganene pofuna kuyambitsa nkhani yomwe anakambirana kale ndi munthuyo pa ulendo wapita. Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene mungakambe komanso mmene mungachitire mbaliyi, onani ndime 12 ndi 13.
9. Kuphunzitsa Anthu: Nkhaniyi iperekedwe kwa munthu wamwamuna kapena wamkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, womuthandiza akhalenso wamkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, womuthandiza akhalenso wamwamuna. (km 5/97 tsa. 2) Wophunzira komanso womuthandizira wake angasankhe kukhala pansi kapena kuimilira. Posonyeza chitsanzo cha phunziro la Baibulo lomwe layamba kale kuchitika, palibe chifukwa chokhalira ndi mawu oyamba kapena omaliza m’chitsanzo chanu. Mungachite zimenezi pokhapokha ngati mwapemphedwa kuti musonyeze mbali zimenezi ina ya mbali zimenezi m’chitsanzo chanu. Si zofunika kuti muchite kuwerenga ndime zonse zimene mwapatsidwa ngakhale kuti mungasankhe kuchita zimenezi.
10. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira: Ngati ikambidwe ngati nkhani, mbali imeneyi ikuyenera kuperekedwa kwa ophunzira wamwamuna. Koma ngati ikhale monga chitsanzo, ingaperekedwe kwa ophunzira wamkazi kapena wamwamuna. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamkazi, womuthandiza akhalenso wamkazi. Ngati yaperekedwa kwa munthu wamwamuna, womuthandiza akhalenso wamwamuna. Wophunzira akuyenera kuyankha momveka bwino komanso mwaluso akamayankha funso la mutu wa nkhani yake kuchokera m’malifalensi amene anapatsidwa. Wophunzira angasankhe kutchula lifalensi imene anagwiritsa ntchito pofufuza kapena ayi pa nthawi imene akukamba nkhani yake.
11. Nkhani: Mbali imeneyi ikuyenera kuperekedwa kwa munthu wamwamuna ndipo izikambidwa mofanana ndi mmene nkhani zimakambidwira kumpingo. Ngati nkhaniyo yachokera pa zakumapeto A m’kabuku ka Muzikonda Anthu, wophunzirayo akuyenera kufotokoza mmene mavesiwo angagwiritsidwire ntchito mu utumiki. Mwachitsanzo, angafotokoze nthawi imene lembalo lingagwiritsidwe ntchito, tanthauzo lake komanso mmene tingaligwiritsire ntchito pokambirana ndi munthu. Ngati nkhani yake ikuchokera pa limodzi mwa phunziro lomwe lili m’kabuku ka Muzikonda Anthu, chidwi chake chizikhala kwambiri pa mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo mu utumiki. Angafotokoze chitsanzo chimene chili pa mfundo yoyambirira m’phunzirolo, kapena angafotokoze Malemba ena owonjezera omwe ali m’phunzirolo ngati kuchita zimenezi kuli kothandiza.
12. Zimene Mungakambe: Mfundo zimene zili m’ndime ino komanso yotsatira zikufotokoza kwambiri za mmene tingachitire pa “Ulendo Woyamba” komanso “Ulendo Obwereza.” Pokhapokha ngati pali kusintha kwina kumene mwauzidwa, cholinga cha ophunzira chiyenera kukhala kufotokoza mfundo zachidule za choonadi cha M’Baibulo zimene zingapindulitsedi munthu amene akulankhula naye. Cholinga china chimakhala kuonetsetsa kuti wapanga maziko womuthandiza kuti adzachezenso ndi munthuyo pa ulendo wina. Wophunzira akuyenera kusankha nkhani yomwe ndi ya panthawi yake komanso yothandiza m’deralo. Angasankhe ngati akufunika kukambirana kuchokera zogawira zathu kapena ngati akufuna kmuonetsa vidiyo kuchokera m’gulu la zinthu zophunzitsira. M’malo mongoloweza zoyenera kunena n’kumalankhula, ophunzira akuyenera kuwonjezera luso lawo lokambirana ndi anthu pokamba nkhani zawo mwaumoyo komanso kumasonyeza chidwi kwa omvetsera.
13. Mtundu wa Ulaliki: Ophunzira akuyenera kugwiritsa ntchito mtundu wa ulaliki umene apatsidwa mogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’dera lanulo. Mwachitsanzo:
(1) Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba: Mtundu wa ulaliki umenewu umaphatikizapo kulalikira khomo ndi khomo kukumana ndi anthu, kuimba ma foni kapenanso kulemba makalata. Zimaphatikizanso kupanga maulendo obwereza kwa anthu amene tinawalalikira.
(2) Kulalikira Mwamwayi: Mtundu wa ulaliki umenewu umaphatikizapo kuyamba kulalikira munthu amene timacheza naye nkhani zina. Ungaphatikizepo kuuza ena mfundo za M’Baibulo, monga amene timakumana nawo kuntchito, kusukulu, kumene timakhala, tikakhala pa ulendo, kapenanso kulikonse komwe tingakumane ndi anthu tikamachita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku.
(3) Kulalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri: Mtundu wa ulaliki umenewu ukuphatikizapo kulalikira pogwiritsira ntchito shelefu, kulalikira anthu pamalo anthu a malonda, ulaliki wa munsewu, kulalikira kumapaki, koimika magalimoto, kapena kulikonse kumene mungapezeko anthu.
14. Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo ndi Mabuku: Kutengera ndi mmene zinthu zilili, wophunzira angasankhe kugwiritsira ntchito zinthu zophunzitsira monga buku kapena vidiyo. Ngati nkhani ya wophunzira ili ndi vidiyo, kapena ngati wophunzirayo wasankha kugwiritsira ntchito vidiyo munkhani yake, iye azingoyerekezera kuti akuonetsa vidiyoyo, kenako azikambirana zimene zili muvidiyoyo. Koma asamamuonetsedi vidiyoyo panthawi ya chitsanzocho.
MOYO WATHU WA CHIKHRISTU
15. Nyimbo ikatha, 15 minitsi yotsatira ya chigawochi izikhala ndi nkhani imodzi kapena ziwiri zothandiza anthu kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu pamoyo wawo. Nkhanizi zingaperekedwe kwa akulu kapena atumiki othandiza oyenerera. Koma mbali ya Zofunika Pampingo iyenera kuperekedwa kwa akulu okha. Munkhani yokambirana, wokamba nkhaniyo angafunse mafunso munkhani yake yonse kuwonjezera pa mafunso amene wapatsidwa munkhaniyo. Mawu oyamba ake akhale achidule pofuna kuti akhale ndi nthawi yambiri yokambirana mfundo zikuluzikulu za munkhaniyo komanso kuti omvetsera atenge nawo mbali mokwanira. Ngati nkhaniyi ikukhudza kufunsa ena mafunso, zingakhale bwino kuti wofunsidwawo abwere papulatifomu m’malo moyankha atakhala pamalo ake.
16. Phunziro la Baibulo la Mpingo: 30 minitsi. Liperekedwe kwa mkulu woyenerera. (M’mipingo yomwe akulu ndi ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapatsidwe mbali imeneyi ngati pakufunika kutero.) Bungwe la akulu likusankha amene angamapatsidwe mbali ya Phunziro la Baibulo la Mpingo. Akulu amene avomerezedwa azikwanitsa kuchititsa bwino phunziroli kuti lizitha panthawi yake, azigogomezera mfundo za m’Malemba amene nkhaniyo yachokera, komanso azithandiza aliyense kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’phunzirolo pa moyo wake. Abale amene asankhidwa kuti azichititsa phunziroli akuyenera kuwerenga ndi kutsatira mfundo zimene gulu lafalitsa zokhudza mmene tingachititsire nkhani yokhala ndi mafunso ndi mayankho (w23.04 tsa. 24, bokosi). Ngati mwamaliza kukambirana mfundo zonse za nkhani ya mlunguwo, palibe chifukwa chotalikitsira phunzirolo pongofuna kumaliza nthawi imene yatsala. Ngati zili zotheka, mlungu uliwonse Phunziro la Baibulo la mpingo lizichititsidwa ndi m’bale wina ndipo m’bale winanso aziwerenga ndime, osati m’bale amene anawerenga mlungu wapita. Ngati tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu wanena kuti phunziroli lichitike mwachidule chifukwa cha nthawi, m’bale amene akuchititsa phunziroli azisankha yekha mmene angalichititsire mwachidule. Iye akhoza kusankha kuti ndime zina zisawerengedwe koma angofunsa mafunso.
MAWU OMALIZA
17. 3 minitsi. Tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu azibwereza mwachidule mfundo zothandiza zimene taphunzira pamsonkhanowo. Mogwirizana ndi nthawi imene yatsala, iye angachite zimenezi popempha omvetsera kuti afotokoze mfundo zothandiza zimene apindula nazo. Akuyeneranso kufotokoza mwachidule zimene mudzaphunzire muwiki yotsatira. Ngati nthawi ilipo angalengezenso maina a anthu amene apatsidwa nkhani muwiki yotsatira. Pokhapokha ngati pali kusintha kumene mwauzidwa, zilengezo zonse zofunika komanso makalata onse opita kumpingo aziwerengedwa ndi tcheyamani akamalankhila mawu ake omaliza. Zilengezo za nthawi zonse, monga zokhudza kulowa mu utumiki wa kumunda kapena kuyeretsa Nyumba ya Ufumu sizikuyenera kulengezedwa, koma zizingoikidwa pabolodi la zilengezo. Ngati muli ndi zilengezo kapena makalata ambiri ndipo mukuona kuti mufunikira nthawi ndithu kuti mumalize, tcheyamani azipempha abale amene ali ndi nkhani za mu Moyo Wathu wa Chikhristu kuti achepetseko nthawi imene agwiritse ntchito. (Onani ndime 16 ndi 19.) Msonkhanowu uzitha ndi nyimbo komanso pemphero.
KUYAMIKIRA NDIPONSO KUPEREKA MALANGIZO
18. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu azimuyamikira ndiponso kumupatsa malangizo kwa nthawi yosapitirira 1 miniti. Malangizowo azichokera paphunziro limene anapatsidwa. Tcheyamani akatchula nkhani imene wophunzira akukamba, asatchulenso phunziro limene wapatsidwa. Koma wophunzirayo akamaliza, tcheyamani ayenera kumuyamikira pogwiritsira ntchito mawu abwino. Iye anganene phunziro limene wophunzirayo anapatsidwa, chifukwa chimene chachititsa wophunzirayo kuti achite bwino, komanso chifukwa chimene akufunikira kupitiriza kuphunzira za mmene angachitire bwino paphunzirolo komanso mmene angachitire zimenezi. Tcheyamani angasankhenso kuyamikira kapena kupereka malangizo pa mbali zina zokhudza mmene wophunzirayo wakambira nkhani yake ngati akuona kuti zingathandize wophunzirayo kapena omvetsera. Tcheyamani angaperekenso malangizo othandiza kwa wophunzira misonkhano ikatha kapena tsiku lina ndipo malangizowo ayenera kuchokera m’kabuku ka Muzikonda Anthu, m’kabuku ka Kuphunzitsa kapena m’buku la Sukulu ya Utumiki. Malangizowo angachokere pa phunziro limene wophunzirayo anapatsidwa kapena pa phunziro lina.—Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya udindo wa tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu ndiponso udindo wa mlangizi wothandiza, onani ndime 19, 24 ndi 25.
KUSUNGA NTHAWI
19. Mbali iliyonse komanso ndemanga za tcheyamani zisapitirire nthawi yake. Ngakhale kuti Kabuku ka Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu kamaikiratu nthawi ya mbali iliyonse, ngati mwamaliza kufotokoza mfundo zonse za mbali yanu simukuyenera kuwonjezera zinthu zina kuti mukwaniritse nthawi yonse yomwe munapatsidwa. Ngati mbali zina za pamisonkhano zapitilira nthawi yake, tcheyamani wa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu kapena Mlangizi wothandiza akuyenera kupereka malangizo kwa amene wapitilira nthawi yakeyo pambuyo pa misonkhano. (Onani ndime 24 ndi 25.) Msonkhano wonse kuphatikiza nyimbo ndi pemphero zisapitirire ola limodzi ndi 45 minitsi.
WOYANG’ANIRA DERA AKAMACHEZERA MPINGO
20. Woyang’anira dera akamachezera mpingo, mapulogalamu aziyenda mmene tasonyezera mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Koma nkhani ya utumiki imene woyang’anira dera amakamba kwa 30 minitsi izilowa m’malo mwa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Nkhani ya utumikiyo isanayambe, tcheyamani ayenera kubwereza zimene taphunzira, kutchula pang’ono zimene tiphunzire mlungu wotsatira, kulengeza zinthu zofunika, kuwerenga makalata ngati alipo kenako kuitana woyang’anira derayo kuti adzakambe nkhani yake. Woyang’anira derayo akamaliza nkhani yake adzauza anthu kuti aimbe nyimbo yomaliza imene iye wasankha. Angathe kupempha m’bale wina kuti apereke pemphero lomaliza. Kalasi B ya m’chinenero cha mpingowo sikuyenera kuchitika muwiki imene woyang’anira dera akuchezera mpingo. Koma gulu la chinenero china la mpingowo lingakhalebe ndi misonkhano muwiki imene woyang’anira dera akuchezera mpingoyo. Koma ikakwana nthawi ya nkhani ya utumiki lachiwiri, gululo lizimvetsera nawo nkhaniyo.
WIKI YA MSONKHANO WADERA KAPENA WACHIGAWO
21. Mukakhala ndi msonkhano wadera kapena wachigawo simuzikhala ndi misonkhano yampingo muwikiyo. Anthu a mumpingo azikumbutsidwa kuti akuyenera kuphunzira mfundo za pamisonkhano ya mpingoyo monga banja kapena pophunzira pawokha.
WIKI YA CHIKUMBUTSO
22. Misonkhano ya mpingo ya mkati mwa wiki sikuyenera kuchitika ngati tsiku la Chikumbutso lilinso mkati mwa wiki.
WOYANG’ANIRA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WA CHIKHRISTU
23. Bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu mmodzi kuti akhale Woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu. Iye azionetsetsa kuti msonkhanowu ukuchitika mwadongosolo komanso motsatira malangizo amene tafotokozawa. Ayeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi mlangizi wothandiza. Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu kakangofika, iye ndi amene azigawa nkhani zonse za misonkhano ya mkati mwa mlungu kwa miyezi iwiri. Zimenezi zikuphatikizapo nkhani za ophunizira, nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunzira komanso amene adzakhale ma tcheyamani kuchokera pa abale amene bungwe la akulu linasankha. (Onani ndime 3-16 ndi 24.) Akamapereka nkhani kwa ophunzira, akuyenera kuganizira zinthu monga: zaka za wophunzirayo, ngati ali wodziwa zambiri kapena ayi komanso ufulu wake wakulankhula pa nkhani imene akukambayo. Akuyeneranso kugwiritsa ntchito mfundo zomwezo akamapereka mbali zina za misonkhanoyi. Aliyense amene wapatsidwa nkhani za ophunzira ayenera kudziwitsidwa kutatsala milungu yosachepera itatu kuti akambe nkhaniyo, pogwiritsa ntchito fomu ya Nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu (S-89). M’bale amene amayang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu ayenera kuonesetsa kuti ndandanda ya misonkhano yonse yaikidwa pa bolodi la mpingo. Bungwe la akulu lingasankhe mkulu wina kapena mtumiki wothandiza kuti azimuthandiza. Komabe akulu okha ndi amene ayenera kugawa nkhani zimene siziperekedwa kwa ophunzira.
TCHEYAMANI WA MSONKHANO WA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WA CHIKHRISTU
24. Wiki iliyonse, mkulu azipemphedwa kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. (Mipingo yomwe ili ndi akulu ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapemphedwe kukhala tcheyamani, ngati pakufunika kutero.) Tcheyamani ndi amene amalankhula mawu oyamba ndi omaliza pamsonkhanowu. Iye ndi amene amaitananso okamba nkhani zosiyanasiyana. Mogwirizana ndi kukula kwa chiwerengero cha akulu ndi atumiki othandiza, iye angakhalenso ndi udindo wochititsa mbali zina. Mbali zake zingakhale monga zimene zili ndi vidiyo imene anthu aonere koma sakambirana chilichonse vidiyoyo ikatha. Mawu amene tcheyamani azilankhula poitana wokamba nkhani wotsatira ayenera kukhala achidule. Bungwe la akulu liyenera kusankha akulu oyenerera kuti azikhala matcheyamani ndipo azisinthanasinthana. Malinga ndi mmene zilili mumpingo wanu, mwina Woyang’anira Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu angamakhale tcheyamani mobwerezabwereza kusiyana ndi akulu ena. Mkulu amene anavomerezedwa kuti azichititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo ndiye kuti ndi woyeneranso kukhala tcheyamani wa msonkhanowu. Mkulu amene wasankhidwa kukhala tcheyamani ayenera kupereka malangizo achikondi komanso kuyamikira abale ndi alongo amene akamba nkhani za ophunzira. Tcheyamani ayenera kuonetsetsanso kuti misonkhano ikutha pa nthawi yake. (Onani ndime 17 ndi 19.) Ngati tcheyamani angakonde komanso ngati papulatifomu pali malo okwanira, iye akhoza kuima pa maikofoni a tcheyamani omwe amaikidwa pambali kuti azilankhula ali pamaikolofoniwa amene akukamba nkhani yotsatira atafika kale pamaikofoni wokambira nkhani. Akhoza kusankhanso kukhala pampando wa papulatifomu panthawi ya mbali za Kuwerenga Baibulo komanso zitsanzo za ophunzira. Izi zingathandize kuti asunge nthawi.
MLANGIZI WOTHANDIZA
25. Udindo wa mlangizi wothandiza ndi kupereka malangizo kwa akulu ndi atumiki othandiza amene akamba nkhani zosiyanasiyana pamisonkhano yonse yampingo. Misonkhanoyi ikuphatikizapo Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu, nkhani ya onse, phunziro la Nsanja ya Olonda komanso phunziro la Baibulo la Mpingo. (Onani ndime 19.)
MAKALASI ENA
26. Mogwirizana ndi chiwerengero cha ophunzira, mipingo ingamakhale ndi makalasi owonjezera. Kalasi iliyonse ikhale ndi woyang’anira woyenerera yemwe ndi mkulu ngati zingatheke. Mtumiki wothandiza woyenerera angagwiritsidwenso ntchito kukalasi B ngati zili zoyenera kutero. Bungwe la akulu liyenera kusankha m’bale kapena abale amene angakhale pa udindo umenewu komanso ngati akuyenera kumasinthana. M’baleyo ayenera kutsatira malangizo amene ali mu ndime 18. Ngati mpingo wanu uzikhala ndi kalasi B, osonkhana ena azipemphedwa kuti apite kukalasi inayo pambuyo pa mbali yakuti Mfundo Zothandiza yomwe ili mu Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu. Iwo ayenera kubwerera kukakhala limodzi ndi mpingo wonse pambuyo pa nkhani yomaliza ya wophunzira.
MAVIDIYO
27. Pamsonkhanowu tizionera mavidiyo amene asankhidwa. Mavidiyo amene tizionera pamsonkhanowu azipezekanso mupulogalamu ya JW Library® ndipo azitheka kuwatsegula pazipangizo zosiyanasiyana.
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
S-38-CN 9/25

