Nahumu 1:1-15

  • Mulungu analanga adani ake (1-7)

    • Mulungu amafuna kuti tizidzipereka kwa iye yekha (2)

    • Yehova amadziwa anthu amene amathawira kwa iye (7)

  • Nineve adzawonongedwa (8-14)

    • Mavuto sadzachitikanso (9)

  • Uthenga wabwino wokhudza Yuda unalengezedwa (15)

1  Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu* wa ku Elikosi:   Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake.+ Yehova amabwezera adani ake,Ndipo adani ake amawasungira mkwiyo.   Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+Koma Yehova salephera kulanga munthu woyenera kulangidwa.+ Njira yake ili mumphepo yowononga ndiponso yamkuntho.Ndipo mitambo ili ngati fumbi lopondapo mapazi ake.+   Amadzudzula nyanja+ ndiponso kuiphwetsa.Ndipo amaumitsa mitsinje yonse.+ Zomera za ku Basana ndi za ku Karimeli zimafota,+Nawonso maluwa a ku Lebanoni amafota.   Mapiri akuluakulu amagwedezeka chifukwa cha iye.Ndipo mapiri angʼonoangʼono amasungunuka.+ Dziko lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha nkhope yakePamodzi ndi nthaka komanso zinthu zonse zokhala mʼdzikomo.+   Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+ Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto,Ndipo miyala idzaphwanyidwa chifukwa cha iye.   Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo pa nthawi yamavuto.+ Amadziwa* amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+   Adzafafaniza mzinda* umenewo ndi madzi osefukira,Ndipo mdima udzathamangitsa adani ake.   Kodi Yehova mungamukonzere chiwembu chotani? Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso. Sipadzakhalanso masautso.+ 10  Iwo alukanalukana ngati minga,Ndipo ali ngati anthu oledzera.Koma adzawotchedwa ngati mapesi ouma. 11  Mwa iwe mudzatuluka winawake amene adzakonzera Yehova chiwembu,Ndiponso kupereka malangizo achabechabe. 12  Yehova wanena kuti: “Ngakhale kuti iwo anali ndi mphamvu zambiri komanso anali ambiri,Adzadulidwa ndipo sadzakhalaponso.* Ndakusautsa,* koma sindidzakusautsanso. 13  Tsopano ndidzathyola goli lake nʼkulichotsa pa iwe,+Ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo. 14  Ponena za iwe,* Yehova walamula kuti,‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako. Ndidzachotsa zifaniziro zosema ndi zifaniziro zachitsulo mʼnyumba* za milungu yako. Ndidzakukonzera manda chifukwa uli ngati chinthu chonyansa.’ 15  Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.Iye akulengeza za mtendere.+ Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza,Chifukwa munthu aliyense wopanda pake sadzadutsa pakati pako. Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Wotonthoza.”
Kapena kuti, “Amasamalira.”
Umenewu ndi mzinda wa Nineve.
Mabaibulo ena amati, “adzadutsa.”
Kutanthauza Yuda.
Kutanthauza Asuri.
Kapena kuti, “mu akachisi.”