Zefaniya 3:1-20

3  Tsoka kwa iye amene akuchita zinthu zopanduka, amene akudziipitsa, mzinda wopondereza anthu ake.+  Mzindawo sunafune kumvera,+ sunalole kulangizidwa,*+ sunakhulupirire Yehova+ ndipo sunayandikire Mulungu wake.+  Akalonga ake anali mikango imene inali kubangula.+ Oweruza ake anali mimbulu yoyenda usiku imene sinatafune mafupa mpaka m’mawa.+  Aneneri ake anali amwano ndi achinyengo.+ Ansembe ake anaipitsa zinthu zopatulika ndipo anaphwanya chilamulo.+  Yehova anali wolungama mkati mwa mzindawo+ ndipo sanali kuchita zosalungama.+ M’mawa uliwonse iye anali kuchita chilungamo chake+ moti sichinali kusowa mpaka m’bandakucha,+ koma wosalungamayo sanali kuchita manyazi.+  “Ine ndinafafaniza mitundu ya anthu ndi kusakaza nsanja zawo za m’makona. Ndinawononga misewu yawo moti simunali kuyendanso munthu. Mizinda yawo inakhala mabwinja ndipo simunatsale munthu aliyense.+  Ndiyeno ndinati, ‘Mosakayikira udzandiopa ndipo udzalola kulangizidwa’+ kuti malo ake okhala asawonongedwe,+ pakuti ndidzamuimba mlandu wa zonsezi.+ Koma zinthu zawo zonse zimene anali kuchita zinali zowawonongetsa ndipo anazichitadi mofulumira.+  “‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,’+ watero Yehova, ‘mpaka tsiku limene ndidzanyamuka kuti ndikaukire ndi kulanda zinthu zofunkhidwa.+ Chigamulo changa ndicho kusonkhanitsa mitundu ya anthu+ ndi kusonkhanitsa pamodzi maufumu kuti ndiwadzudzule mwamphamvu+ ndi kuwatsanulira mkwiyo wanga wonse woyaka moto, pakuti moto wa mkwiyo wanga udzanyeketsa dziko lonse lapansi.+  Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera+ kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova+ ndi kumutumikira mogwirizana.’*+ 10  “Anthu amene akundichonderera, anthu anga obalalitsidwa, adzandibweretsera mphatso kuchokera kuchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+ 11  Pa tsiku limenelo, sudzachita manyazi chifukwa cha zochita zako zimene unandilakwira nazo,+ pakuti ndidzachotsa pamaso pako anthu odzikweza amene amakhala mosangalala+ ndipo sudzakhalanso wodzikweza m’phiri langa lopatulika.+ 12  Mwa iwe ndidzasiyamo anthu ena, odzichepetsa ndi ofatsa,+ ndipo amenewa adzapeza chitetezo m’dzina la Yehova.+ 13  Otsala mwa Isiraeli+ sadzachita zinthu zosalungama+ kapena kunena bodza.+ Sadzakhala ndi lilime lachinyengo+ koma iwo adzadya ndi kugona pansi momasuka+ ndipo sipadzakhala wowaopsa.”+ 14  Fuula mosangalala iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuula mokondwera+ iwe Isiraeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!+ 15  Yehova wachotsa zigamulo zake pa iwe.+ Watembenuza ndi kubweza mdani wako.+ Mfumu ya Isiraeli, Yehova, ali pakati pa anthu ako+ ndipo sudzaopanso kuti tsoka likugwera.+ 16  Tsiku limenelo Yerusalemu adzauzidwa kuti: “Usaope iwe Ziyoni+ ndipo usalefuke.+ 17  Yehova Mulungu wako ali pakati pa anthu ako ndipo adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu.+ Iye adzakondwera nawe.+ Adzakhala phee chifukwa chokhutira ndi chikondi chimene akukusonyeza, ndipo adzafuula mosangalala chifukwa chokondwera nawe. 18  “Anthu ogwidwa ndi chisoni+ amene sanapezeke pa zikondwerero zako ndidzawasonkhanitsa pamodzi.+ Iwo sanali ndi iwe chifukwa anali kudziko lachilendo kumene anali kutonzedwa.+ 19  Pa nthawi imeneyo ndidzaukira onse amene akukuzunza+ ndipo ndidzapulumutsa otsimphina.+ Anthu obalalitsidwa ndidzawasonkhanitsa pamodzi+ ndipo ndidzawachititsa kukhala otamandidwa komanso otchuka m’dziko lonse limene anachititsidwa manyazi. 20  Pa nthawi imeneyo ndidzakubwezaninso kunyumba anthu inu. Ndithu, pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani pamodzi. Ndidzakuchititsani kukhala otchuka komanso otamandidwa pakati pa mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi. Zimenezi zidzachitika ndikadzabwezeretsa pamaso pako anthu ako amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo,” watero Yehova.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Mawu ake enieni, “azimutumikira phewa ndi phewa.”