Zefaniya 2:1-15

2  Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi,+ inu anthu a mtundu wopanda manyazi.+  Lamulo lisanayambe kugwira ntchito,+ tsiku lisanadutse ngati mankhusu,* mkwiyo woyaka moto wa Yehova usanakugwereni anthu inu,+ tsiku la mkwiyo wa Yehova lisanakufikireni,+  bwerani kwa Yehova,+ inu nonse ofatsa a padziko lapansi,+ amene mwakhala mukutsatira zigamulo zake. Yesetsani kukhala olungama,+ yesetsani kukhala ofatsa.+ Mwina+ mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+  Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,+ ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+ Kunena za Asidodi,+ anthu ake adzawathamangitsa dzuwa lili paliwombo,+ ndipo Ekironi adzazulidwa.+  “Tsoka kwa anthu okhala m’chigawo cha m’mphepete mwa nyanja, mtundu wa Akereti.+ Yehova wakudzudzulani anthu inu. Iwe Kanani, dziko la Afilisiti, nawenso ndidzakuwononga, kotero kuti m’dziko lako simudzatsala munthu aliyense.+  Chigawo cha m’mphepete mwa nyanja chidzakhala malo odyetserako ziweto,+ malo okhala ndi zitsime za abusa ndiponso malo a makola amiyala a nkhosa.  Chigawo chimenecho chidzakhala cha otsala a m’nyumba ya Yuda+ ndipo adzapezamo msipu. Madzulo iwo adzagona momasuka m’nyumba za mu Asikeloni. Zidzatero chifukwa chakuti Yehova Mulungu wawo adzawakumbukira+ ndipo adzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu awo omwe anagwidwa n’kutengedwa kupita ku ukapolo.”+  “Ndamva chitonzo cha Mowabu+ ndi mawu onyoza a ana a Amoni+ amene anali kunena kwa anthu anga. Iwo anali kuopseza anthu anga modzitukumula kuti awalanda dziko lawo.”  Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ Mowabu adzakhala ndendende ngati Sodomu,+ ndipo ana a Amoni+ adzakhala ngati Gomora, malo odzaza zomera zoyabwa ndiponso mchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.*+ Otsala mwa anthu anga adzafunkha zinthu zawo, ndipo otsala a mtundu wa anthu anga adzawagwira ukapolo.+ 10  Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+ komanso chifukwa chakuti anali kunyoza ndi kudzikweza pamaso pa anthu a Yehova wa makamu.+ 11  Yehova adzawachititsa mantha,+ pakuti adzawondetsa milungu yonse ya padziko lapansi.+ Pamenepo anthu adzamugwadira,+ aliyense pamalo pake, zilumba zonse za mitundu ya anthu zidzamugwadira.+ 12  “Inunso Aitiyopiya+ mudzaphedwa ndi lupanga langa.+ 13  “Iye adzatambasulira dzanja lake kumpoto ndipo adzawononga Asuri.+ Adzachititsa Nineve kukhala bwinja,+ kukhala dziko lopanda madzi ngati chipululu. 14  Magulu a nyama, nyama zakutchire za m’deralo zidzagona momasuka pakati pa mzindawo.+ Nungu ndiponso mbalame ya vuwo+ zidzagona usiku wonse pakati pa zipilala zakugwa za mzindawo.+ Pawindo padzamveka mawu a nyimbo. Pamakomo a nyumba padzakhala zibuma za nyumba zakugwa, pakuti iye adzakanganula matabwa oyalidwa kukhoma.*+ 15  Mzinda uwu unali wosangalala ndipo unkakhala mosaopa chilichonse.+ Mumtima mwake unali kunena kuti, ‘Ndilipo ndekha, ndipo palibe wondiposa.’+ Mzindawu wakhala chinthu chodabwitsa, malo amene nyama zakutchire zimagonamo momasuka. Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawu adzaimba mluzu ndipo adzapukusa mutu.”+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”