Yuda 1:1-25

 Ine Yuda, kapolo wa Yesu Khristu koma m’bale wake wa Yakobo,+ ndikulembera oitanidwa+ okondedwa ndi Mulungu Atate, amene ali naye pa ubwenzi,+ amenenso asungidwa+ kuti akhale ogwirizana ndi Yesu Khristu.  Chifundo,+ mtendere,+ ndi chikondi+ ziwonjezeke kwa inu.+  Okondedwa,+ ngakhale kuti ndinali kuyesetsa kuti ndikulembereni za chipulumutso chimene tonsefe tili nacho,+ ndaona kuti ndi bwino kuti ndikulembereni zokulimbikitsani kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro+ chomwe chinaperekedwa kamodzi kokha kwa oyerawo.+  Ndatero chifukwa chakuti anthu ena alowa mozemba pakati pathu.+ Anthu amenewa Malemba anawasonyezeratu kalekale+ kuti adzaweruzidwa.+ Iwo ndiwo anthu osaopa Mulungu+ amene atenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lotayirira,+ ndipo akhala osakhulupirika+ kwa Ambuye wathu mmodzi yekha+ amene anatigula,+ Yesu Khristu.  Ngakhale kuti mukudziwa kale zinthu zonse, ndikufuna kukukumbutsani kuti,+ ngakhale kuti Yehova anapulumutsa anthu ake powatulutsa m’dziko la Iguputo,+ pambuyo pake anawononga amene analibe chikhulupiriro.+  Ndiponso angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala,+ Mulungu anawasunga kosatha m’maunyolo,+ mu mdima wandiweyani kuti adzaweruzidwe pa tsiku lalikulu.+  Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+  Ngakhale zili choncho, anthu amenewanso, pokonda zongolota,+ akuipitsa matupi ndi kunyalanyaza ulamuliro+ ndipo amalankhula zonyoza amene ali ndi ulemerero.+  Koma pamene Mikayeli+ mkulu wa angelo+ anasemphana maganizo+ ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose,+ sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza,+ m’malomwake anati: “Yehova akudzudzule.”+ 10  Koma anthu amenewa amalankhula monyoza zinthu zonse zimene sakuzidziwa bwinobwino,+ ndipo ali ngati nyama zopanda nzeru. Pochita zinthu zawo zonse zimene amazichita mwachibadwa, amakhala ngati nyama+ ndipo mwa kutero amapitiriza kudziipitsa.+ 11  Tsoka kwa iwo, chifukwa chakuti ayenda m’njira ya Kaini.+ Athamangira m’njira yolakwika ya Balamu+ kuti alandire mphoto, ndipo awonongeka potengera kulankhula kopanduka+ kwa Kora.+ 12  Anthu amenewa ali ngati miyala ikuluikulu yobisika m’madzi,+ pamene akudya nanu limodzi pa maphwando anu amene mumachita kuti musonyezane chikondi. Alinso ngati abusa amene amadzidyetsa okha mopanda mantha,+ mitambo yopanda madzi yotengeka+ ndi mphepo+ kupita uku ndi uku, mitengo yopanda zipatso koma nyengo yake yobereka zipatso ili pafupi kutha, yakufa kawiri, yozulidwa.+ 13  Ali ngatinso mafunde oopsa a panyanja otulutsa thovu la zinthu zoyenera kuwachititsa manyazi,+ ndiponso nyenyezi zosochera, zimene azisungira mdima wandiweyani wosatha.+ 14  Ngakhalenso Inoki,+ wa m’badwo wa 7 kuchokera kwa Adamu, analosera za iwowa pamene anati: “Taonani! Yehova anabwera ndi miyandamiyanda ya oyera ake,*+ 15  kudzapereka chiweruzo kwa onse,+ ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu, komanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.”+ 16  Anthu amenewa ndi okonda kung’ung’udza,+ okonda kudandaula za moyo wawo, ongotsatira zilakolako zawo,+ ndipo amalankhula modzitukumula.+ Amatamandanso anthu ena+ n’cholinga choti apezepo phindu. 17  Koma inu okondedwa, kumbukirani mawu amene atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu ananena kalero,+ 18  mmene anali kukuuzani kuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola, otsatira zilakolako zawo pa zinthu zonyoza Mulungu.”+ 19  Anthu amenewa ndiwo amayambitsa magawano,+ amachita zauchinyama,+ ndipo alibe mzimu wa Mulungu.+ 20  Koma inu okondedwa, podzilimbitsa+ pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana,+ ndi kupemphera mu mphamvu ya mzimu woyera,+ 21  pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.+ Chitani zimenezi pamene mukuyembekezera kuti chifundo+ cha Ambuye wathu Yesu Khristu chidzakutsegulireni njira yoti mulandirire moyo wosatha.+ 22  Ndiponso, pitirizani kuchitira chifundo+ ena amene akukayikakayika.+ 23  Apulumutseni+ mwa kuwakwatula pamoto.+ Pitirizaninso kuchitira chifundo ena onse, koma ndi mantha. Iwo aipitsa zovala zawo zamkati ndi ntchito za thupi. Choncho pamene mukuwachitira chifundo, mutalikirane kwambiri ndi zovala zawo zoipitsidwazo.+ 24  Koma ponena za Mulungu amene angathe kukutetezani+ kuti musapunthwe, ndiponso kukuikani opanda chilema+ pamaso pa ulemerero wake ndi chisangalalo chachikulu, 25  kwa iyeyo, Mulungu yekhayo amenenso ndi Mpulumutsi wathu+ mwa Yesu Khristu+ Ambuye wathu, kukhale ulemerero,+ ukulu, mphamvu+ ndi ulamuliro,+ kuchokera kalekale+ kufikira panopa, mpaka ku nthawi yonse yomka muyaya.+ Ame.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “masauzande makumimakumi a oyera ake.”