Yoswa 9:1-27

9  Mafumu+ a kutsidya kwa Yorodano anamva zimene zinachitika. Amenewa anali mafumu a Ahiti,+ Aamori, Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi ndi Ayebusi.+ Iwo anali kukhala kudera lamapiri, ndiponso ku Sefela, ndi m’mbali monse mwa Nyanja Yaikulu,+ komanso pafupi ndi Lebanoni.+ Mafumu onsewo atangomva zimene zinachitikazo,  anasonkhanitsa pamodzi magulu awo ankhondo kuti amenyane ndi Yoswa ndi Isiraeli.+  Anthu a ku Gibeoni+ anamva zimene Yoswa anachita ku Yeriko+ ndi Ai.+  Atamva choncho, paokha anachitapo kanthu mwanzeru.+ Ananyamula chakudya m’matumba akutha n’kukweza pa abulu awo. Ananyamulanso vinyo m’matumba achikopa akutha, omangamanga mong’ambika.+  Anavala nsapato zakutha zosokererasokerera, ndi zovala zansanza. Mkate wawo wonse wa kamba wa pa ulendo unali wouma ndi wofumbutuka.  Kenako anapita kwa Yoswa kumsasa wa ku Giligala,+ ndipo anauza iye ndi amuna achiisiraeli kuti: “Ife tachokera kudziko lakutali kwambiri. Chonde, chitani nafe pangano.”+  Koma amuna achiisiraeli anayankha Ahiviwo+ kuti: “Mwinamwake mumakhala pafupi chakonkuno. Ndiye tingachite nanu bwanji pangano?”+  Iwo poyankha anauza Yoswa kuti: “Ndife okonzeka kukhala akapolo anu.”+ Ndiyeno Yoswa anawafunsanso kuti: “Koma ndinu ndani makamaka, ndipo mwachokera kuti?”  Iwo anamuyankha kuti: “Akapolo anufe tachokera kudziko lakutali kwambiri.+ Tabwera chifukwa tamva za dzina+ la Mulungu wanu, Yehova. Tamva mbiri yake ndi zonse zimene anachita ku Iguputo.+ 10  Tamvanso zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kutsidya lina la Yorodano. Mafumuwo ndiwo Sihoni+ mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali ku Asitaroti.+ 11  Pakumva zimenezi, akulu akwathu ndi anthu onse a m’dziko lathu anatiuza kuti,+ ‘Tengani kamba wa pa ulendo, mupite mukakumane nawo. Mukawauze kuti: “Ife ndife akapolo anu.+ Chonde chitani nafe pangano.”’+ 12  Tsiku limene tinanyamuka kunyumba kubwera kwa inu, mkate wathuwu umene tinautenga monga kamba wa pa ulendo unali wotentha. Koma taonani! Tsopano wauma ndipo ukufumbutuka.+ 13  Taonaninso matumba achikopa a vinyowa. Matumba amenewa anali atsopano pamene timathiramo vinyo, koma tsopano atha ndi kung’ambika.+ Komanso onani zovala zathu ndi nsapato zathuzi, zang’ambika chifukwa cha kutalika kwa ulendo.” 14  Pamenepo amuna achiisiraeli anatengako zakudyazo kuti aziyang’anitsitse, ndipo sanafunsire kwa Yehova.+ 15  Choncho Yoswa anagwirizana nawo za mtendere,+ ndipo anachita nawo pangano kuti asawaphe. Zitatero, atsogoleri+ a Isiraeli analumbira kwa anthuwo.+ 16  Koma patapita masiku atatu atachita nawo panganolo, anamva kuti anthuwo anali apafupi, ndi kuti anali kukhala m’dera lomwelo. 17  Pamenepo Aisiraeliwo ananyamuka n’kukafika kumizinda ya anthuwo pa tsiku lachitatu. Mizindayo inali Gibeoni,+ Kefira,+ Beeroti,+ ndi Kiriyati-yearimu.+ 18  Ana a Isiraeli sanawaphe anthuwo. Sanawaphe chifukwa atsogoleri a khamu la ana a Isiraeli anali atalumbirira+ anthuwo pali Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ Choncho, khamu lonse linayamba kung’ung’udza motsutsana ndi atsogoleriwo.+ 19  Pamenepo atsogoleri onse anauza khamu lonselo kuti: “Ife tinawalumbirira pali Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndipo tsopano sitingawachitire choipa.+ 20  Tiwasiya kuti akhale ndi moyo, kuti Mulungu asatikwiyire chifukwa cha lumbiro limene tinawalumbirira.”+ 21  Ndiyeno atsogoleriwo anawauza kuti: “Akhale ndi moyo, ndipo akhale otola nkhuni ndi otungira madzi khamu lonse la Isiraeli,+ monga mmene tinawalonjezera.”+ 22  Pambuyo pake Yoswa anaitana anthuwo, n’kuwafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani munatipusitsa ponena kuti ‘Timakhala kutali kwambiri ndi inu,’+ pamene mukukhala nafe pafupi chonchi?+ 23  Tsopano mukhala anthu otembereredwa.+ Mukhala akapolo+ otola nkhuni ndi otungira madzi nyumba ya Mulungu wanga ku nthawi yonse.”+ 24  Anthuwo anamuyankha Yoswa kuti: “Akapolo anufe tinachita zimenezi+ chifukwa tinali ndi mantha aakulu.+ Tinachita mantha titauzidwa mosapita m’mbali za Yehova Mulungu wanu. Tinamva kuti analamula mtumiki wake Mose kuti akupatseni dziko lonse lino, ndi kuti muphe anthu onse okhalamo.+ 25  Tsopano tadzipereka m’manja mwanu. Muchite nafe chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino ndi choyenera kwa inu.”+ 26  Yoswa anavomereza kuchita nawo motero. Anawalanditsa kwa ana a Isiraeli kuti asawaphe.+ 27  Chotero pa tsikuli, Yoswa anawaika+ kukhala otola nkhuni ndi otungira madzi Aisiraeli,+ ndiponso kuti azitola nkhuni ndi kutunga madzi a paguwa lansembe la Yehova, pamalo alionse amene Mulungu wasankha.+ Iwo akhala akuchita zimenezi mpaka lero.

Mawu a M'munsi