Yoswa 8:1-35

8  Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Usaope kapena kuchita mantha.+ Tenga amuna onse ankhondo. Nyamuka, upite kudziko la Ai. Taona, mfumu ya Ai ndaipereka m’manja mwako limodzi ndi anthu ake, mzinda wake, ndi dziko lake.+  Ukachite kwa Ai ndi mfumu yake zimene unachita kwa Yeriko ndi mfumu yake.+ Koma katundu ndi ziweto za mumzindawo mukafunkhe zikakhale zanu.+ Usankhe amuna ena oti akabisale kumbuyo kwa mzindawo.”+  Choncho, Yoswa limodzi ndi amuna onse ankhondo+ anakonzeka kupita ku Ai. Yoswa anasankha amuna okwanira 30,000, asilikali amphamvu ndi olimba mtima,+ n’kuwatumiza usiku.  Anawalamula kuti: “Inu mukabisale+ kumbuyo kwa mzindawo. Musakakhale patali kwambiri ndi mzindawo, ndipo nonsenu mukakhale okonzeka.  Koma ine ndi onse amene akakhale ndi ine, tikafika pafupi kwambiri ndi mzindawo. Iwo akakatuluka kuti adzamenyane nafe ngati poyamba paja,+ tikathawa.  Akakaona choncho, akatithamangitsa. Ife tikathawa kuti tikawatulutse mpaka atafika kutali ndi mzindawo, pakuti adzati, ‘Akuthawa ngati poyamba paja.’+  Zikakatero, inu mukavumbuluke ndi kukalanda mzindawo, pakuti Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu m’manja mwanu.+  Ndipo mukakangoti mwalanda mzindawo, mukauyatse moto.+ Mukachite zimenezo malinga ndi mawu a Yehova. Izi n’zimene ndakulamulani.”+  Pambuyo pake Yoswa anawatumiza amunawo, ndipo iwo anapita kumalo okabisalako. Kumeneko anakamanga timisasa tobisalira, kumadzulo kwa Ai. Anamanga timisasato pakati pa Ai ndi Beteli. Koma usikuwo Yoswa anagona limodzi ndi asilikali amene anali nawo. 10  Kenako, Yoswa anadzuka m’mawa kwambiri+ n’kuyendera asilikali ake. Atatero ananyamuka, iye limodzi ndi akulu a Isiraeli, n’kutsogolera asilikaliwo ku Ai. 11  Ankhondo onse+ amene anali limodzi ndi Yoswa anapita naye, n’kukafika pafupi ndi mzindawo kutsogolo kwake. Atafika anamanga msasa kumpoto kwa Ai, ndipo pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12  Tsopano anatenga amuna pafupifupi 5,000, nawabisa+ pakati pa Beteli+ ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda wa Ai. 13  Choncho asilikaliwo anakhazikitsa msasa wawo waukulu kumpoto kwa mzindawo,+ ndipo wina anaukhazikitsa kumadzulo,+ kumbuyo kwenikweni kwa mzindawo. Usikuwo Yoswa ananyamuka n’kupita pakati pa chigwacho. 14  Tsopano mfumu ya Ai itangoona zimenezo, amuna a mumzindawo anakonzekera msangamsanga. M’mawa mwake analawirira kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Mfumuyo limodzi ndi anthu ake onse, ananyamuka pa nthawi imene anapangana, ndipo analowera kuchigwa cha m’chipululu. Koma mfumuyo sinadziwe kuti asilikali ena anali atabisala kumbuyo kwa mzindawo.+ 15  Pofuna kuonetsa ngati akugonja, Yoswa limodzi ndi Aisiraeli onse amene anali naye+ anathawa kudzera njira yolowera kuchipululu.+ 16  Zitatero, anthu onse a mumzindawo anaitanidwa kuti akathamangitse Aisiraeli. Anthuwo anathamangitsa Aisiraeliwo limodzi ndi Yoswa, mpaka anafika kutali ndi mzinda wawo.+ 17  Panalibe mwamuna ndi mmodzi yemwe amene anatsala mu Ai ndi m’Beteli. Onse anapita kukathamangitsa Aisiraeli, moti zipata za mzindawo anangozisiya zosatseka. 18  Tsopano Yehova anauza Yoswa kuti: “Lozetsa nthungo* imene ili m’dzanja lako ku Ai,+ pakuti mzindawo ndaupereka m’manja mwako.”+ Chotero Yoswa analozetsa kumzindawo nthungo imene inali m’dzanja lake. 19  Pamenepo, asilikali amene anabisala aja anavumbuluka pamalo pamene anali. Pa nthawi imene iye anatambasula dzanja lake, iwo anathamanga n’kukalowa mumzindawo n’kuulanda.+ Atatero, anauyatsa moto mzindawo mofulumira.+ 20  Amuna a ku Ai atacheuka anangoona utsi uli tolo mumzindawo, ndipo anasoweratu mphamvu zoti n’kuthawira kwina kulikonse. Pamenepo asilikali achiisiraeli amene ankathawira kuchipululu aja, anatembenukira amuna a ku Aiwo. 21  Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye ataona kuti asilikali omwe anabisala+ aja alanda mzindawo, ndiponso utsi ukufuka mumzindawo, anatembenukira amuna a ku Ai n’kuyamba kuwapha. 22  Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Chotero amuna a ku Ai anakhala pakati pa Aisiraeli, ena mbali iyi, ena mbali inayo. Pamenepo Aisiraeli anapha amuna a ku Ai, moti panalibe wotsala ndi moyo kapena wothawa.+ 23  Koma mfumu+ ya Ai anaigwira, n’kubwera nayo yamoyo kwa Yoswa. 24  Aisiraeli anapitiriza kupha amuna ankhondo onse a ku Ai. Anawaphera kuchipululu kumene anthu a ku Aiwo anathamangitsirako Aisiraeli. Anawapha ndi lupanga mpaka kuwatha onse. Atatero, Aisiraeliwo anabwerera ku Ai, n’kukapha ndi lupanga ena onse otsala. 25  Anthu onse amene anaphedwa tsikulo, amuna ndi akazi, anakwana 12,000, anthu onse a ku Ai. 26  Ndipo Yoswa sanatsitse mkono wake umene anautambasula polozetsa nthungo+ kumzindawo, mpaka anthu onse a ku Ai ataphedwa.+ 27  Koma Aisiraeliwo anafunkha ziweto ndi katundu wa mumzindawo n’kukhala zawo, malinga ndi zimene Yehova analamula Yoswa.+ 28  Chotero Yoswa anatentha mzinda wa Ai+ n’kuusiya uli bwinja lokhalapo mpaka kalekale, ndipo lilipobe mpaka lero. 29  Ndipo mfumu ya Ai+ anaipachika pamtengo mpaka madzulo.+ Koma dzuwa litatsala pang’ono kulowa, Yoswa analamula kuti achotse mtembo wa mfumuyo+ pamtengopo. Atauchotsa mtembowo anakauponya pachipata cha mzindawo, n’kuufotsera ndi mulu waukulu wa miyala, ndipo muluwo ulipo mpaka lero. 30  Inali nthawi imeneyi pamene Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Isiraeli guwa lansembe+ m’phiri la Ebala.+ 31  Anamanga guwalo mogwirizana ndi zimene Mose mtumiki wa Yehova analamula ana a Isiraeli, monga mwa zolembedwa m’buku la chilamulo+ cha Mose, zimene zimati: “Guwa lansembe la miyala yathunthu, yosasema ndi chipangizo chachitsulo.”+ Ndipo iwo anaperekerapo kwa Yehova nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano.+ 32  Kenako, Yoswa analemba pamiyala+ chilamulo chimene Mose analembera ana a Isiraeli.+ 33  Aisiraeli onse, atsogoleri awo,+ akapitawo awo, ndi oweruza awo anasonkhanitsidwa pamodzi. Panalinso alendo okhala pakati pawo.+ Ena anaima mbali iyi ya Likasa, ena anaima mbali inayo, pamaso pa ansembe+ achilevi. Ansembewo anali atanyamula likasa la pangano la Yehova.+ Hafu ya anthuwo inaima m’phiri la Gerizimu,+ ndipo hafu ina inaima m’phiri la Ebala,+ (monga mmene Mose mtumiki wa Yehova analamulira,)+ kuti Aisiraeliwo adalitsidwe+ choyamba. 34  Pambuyo pake, Yoswa anawerenga mokweza mawu onse a chilamulo,+ madalitso+ ndi matemberero,+ malinga ndi zonse zolembedwa m’buku la chilamulo. 35  Panalibe ngakhale liwu limodzi pamawu onse amene Mose analamula, limene Yoswa sanaliwerenge mokweza pamaso pa mpingo wonse wa Aisiraeli.+ Akazi+ ndi ana aang’ono,+ komanso alendo okhala pakati pawo+ anali pomwepo.

Mawu a M'munsi

Tikati “nthungo” tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.