Yoswa 4:1-24

4  Mtundu wonse utangotha kuwoloka mtsinje wa Yorodano,+ Yehova anauza Yoswa kuti:  “Tenga amuna 12 pakati pa anthuwa, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+  Uwalamule kuti, ‘Pitani pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene ansembe anaimapo chilili,+ mukanyamulepo miyala 12.+ Muisenze ndi kukaiika kumene mugone+ usiku wa lero.’”  Choncho Yoswa anaitana amuna 12+ amene anawasankha pakati pa ana a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.  Ndipo anawauza kuti: “Dutsani kutsogolo kwa likasa la Yehova Mulungu wanu, mukafike pakati pa mtsinje wa Yorodano. Aliyense akanyamule mwala umodzi paphewa pake, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Isiraeli.  Miyala imeneyo idzakhala chizindikiro pakati panu.+ Ana anu akamadzafunsa m’tsogolo muno kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+  Muzidzawauza kuti, ‘N’chifukwa chakuti madzi a mumtsinje wa Yorodano anadukana pamaso pa likasa la pangano la Yehova.+ Likasalo litadutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinje wa Yorodanowo anadukana, ndipo miyala imeneyi ndi chikumbutso cha zimenezo kwa ana a Isiraeli mpaka kalekale.’”*+  Chotero ana a Isiraeliwo anachita monga mmene Yoswa anawalamulira. Anapita pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo anakanyamula miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Isiraeli,+ monga mmene Yehova analamulira Yoswa. Ananyamula miyalayo ndi kukaiika kumalo awo ogona.+  Panalinso miyala ina 12 imene Yoswa anaisanjikiza pakati pa mtsinje wa Yorodano, pamalo amene anaimapo+ ansembe onyamula likasa la pangano. Miyalayo ilipo mpaka lero. 10  Ansembe onyamula Likasawo, anaimabe chiimire pakati+ pa mtsinje wa Yorodano, kufikira zitachitika zonse zimene Yehova analamula Yoswa kuti auze anthuwo, mogwirizana ndi zonse zimene Mose analamula Yoswa.+ Ansembewo ali chiimire choncho, anthuwo anawoloka mtsinjewo mofulumira.+ 11  Anthu onse atangotha kuwoloka, likasa+ la Yehova linawoloka litanyamulidwa ndi ansembewo pamaso pa anthuwo. 12  Ana a Rubeni ndi ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase,+ anawoloka pamaso pa ana a Isiraeli atafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo,+ monga mmene Mose anawauzira.+ 13  Amuna onyamula zida okwanira pafupifupi 40,000, anawoloka pamaso pa Yehova kukamenya nkhondo m’chipululu cha Yeriko. 14  Pa tsikuli, Yehova anachititsa Yoswa kukhala wamkulu m’maso mwa Aisiraeli onse,+ ndipo anayamba kumuopa monga mmene anaopera Mose masiku onse a moyo wake.+ 15  Yehova anauza Yoswa kuti: 16  “Lamula ansembe onyamula likasa la umboni+ kuti atuluke mumtsinje wa Yorodano.” 17  Chotero Yoswa analamula ansembewo, kuti: “Tulukani mumtsinje wa Yorodano.” 18  Ansembe onyamula likasa+ la pangano la Yehova atatuluka pakati pa mtsinje wa Yorodano, ndipo mapazi+ awo ataponda kumtunda, madzi a mtsinjewo anayamba kubwerera mwakale, ndipo anasefukira+ mbali zonse ngati poyamba. 19  Anthuwo anawoloka mtsinje wa Yorodano pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, ndipo anakamanga msasa ku Giligala,+ kumalire a kum’mawa kwa Yeriko. 20  Miyala 12 imene iwo anaitenga mumtsinje wa Yorodano ija, Yoswa anaisanjikiza ku Giligala.+ 21  Kenako anauza ana a Isiraeli kuti: “Ana anu akamadzafunsa abambo awo m’tsogolomu kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22  Muzidzawauza ana anuwo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodanowu panthaka youma.+ 23  Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pawo, kufikira iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo pamaso pathu, mpaka tonse titawoloka.+ 24  Yehova anachita zimenezi kuti mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi idziwe kuti dzanja lake+ ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muzimuopadi Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.