Yoswa 24:1-33

24  Ndiyeno Yoswa anasonkhanitsa pamodzi mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu.+ Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli,+ atsogoleri, oweruza, ndi akapitawo, ndipo iwo anaima pamaso pa Mulungu woona.+  Tsopano Yoswa anauza anthu onse kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Kalekale, makolo anu,+ kuphatikizapo Tera, bambo ake a Abulahamu ndi Nahori,+ ankakhala kutsidya lina la Mtsinje,*+ ndipo ankatumikira milungu ina.  “‘Patapita nthawi, ndinatenga Abulahamu+ tate wanu, kuchokera kutsidya lina la Mtsinje,+ ndipo ndinamuyendetsa m’dziko lonse la Kanani, ndi kuchulukitsa mbewu yake.+ Chotero ndinam’dalitsa ndipo anabereka Isaki,+  Isaki anabereka Yakobo ndi Esau.+ Pambuyo pake Esau ndinam’patsa phiri la Seiri kuti likhale lake.+ Kenako, Yakobo ndi ana ake anapita ku Iguputo.+  Patapita nthawi, ndinatumiza Mose ndi Aroni,+ ndipo ndinagwetsera Iguputo miliri.+ Nditatero ndinakutulutsani+ ku Iguputoko.  Pamene ndinali kutulutsa makolo anu ku Iguputo,+ atatsala pang’ono kufika kunyanja, Aiguputo anawathamangira+ ndi magaleta ankhondo ndiponso amuna okwera pamahatchi, mpaka ku Nyanja Yofiira.  Pamenepo, iwo anayamba kufuulira Yehova.+ Choncho ine ndinaika mdima pakati pa iwo ndi Aiguputuwo,+ ndipo ine ndinawamiza ndi madzi a m’nyanja.+ Munaona ndi maso anu zimene ndinachita ku Iguputo.+ Kenako, inu munakhala m’chipululu masiku ambiri.+  “‘Pamapeto pake, ndinakufikitsani kudziko la Aamori amene anali kukhala kutsidya lina la Yorodano. Iwo anayamba kumenyana nanu,+ koma ine ndinawapereka m’manja mwanu kuti mutenge dziko lawo kukhala lanu. Chotero ndinawafafaniza kuwachotsa pamaso panu.+  Kenako Balaki mwana wa Zipori,+ mfumu ya Mowabu, ananyamuka kukamenyana ndi Isiraeli.+ Iye anaitanitsa Balamu, mwana wa Beori, ndi kumuuza kuti akutemberereni.+ 10  Ine sindinafune kumvera Balamu.+ Chotero, iye anakudalitsani mobwerezabwereza,+ ndipo ine ndinakulanditsani m’manja mwake.+ 11  “‘Kenako munawoloka Yorodano+ n’kufika ku Yeriko.+ Nzika za ku Yeriko, Aamori, Aperezi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi anayamba kumenyana nanu, koma ine ndinawapereka m’manja mwanu.+ 12  Ndinawachititsa mantha inu musanafike, choncho anakuthawani+ monga anachitira mafumu awiri a Aamori. Iwo sanathawe chifukwa cha lupanga lanu kapena chifukwa cha uta wanu.+ 13  Chotero ndinakupatsani dziko limene simunakhetsere thukuta ndi mizinda imene simunamange,+ ndipo inu munayamba kukhalamo. Ndiponso mukudya zipatso za mitengo ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunabzale.’+ 14  “Tsopano opani Yehova+ ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo,+ ndipo tumikirani Yehova. 15  Ngati kutumikira Yehova kukukuipirani, sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira,+ kaya milungu imene makolo anu amene anali kutsidya lina la Mtsinje anatumikira,+ kapena milungu ya Aamori amene mukukhala m’dziko lawo.+ Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”+ 16  Pamenepo, anthuwo anayankha kuti: “Sitingayerekeze kusiya Yehova, kuti tizitumikira milungu ina. 17  Pakuti ndi Yehova Mulungu wathu amene anatitulutsa m’dziko la Iguputo+ pamodzi ndi makolo athu, kutichotsa m’nyumba yaukapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza m’njira yonse imene tinayenda, ndiponso kwa mitundu yonse ya anthu amene tinadutsa pakati pawo.+ 18  Yehova anathamangitsa mitundu yonse ya anthu+ pamaso pathu, ngakhale Aamori amene anali kukhala m’dzikoli. Choncho, nafenso tizitumikira Yehova chifukwa iye ndi Mulungu wathu.”+ 19  Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+ 20  Mukasiya Yehova+ n’kuyamba kutumikira milungu yachilendo,+ iyenso adzakutembenukirani ndithu, n’kukuchitirani zoipa ndi kukufafanizani, pambuyo pokuchitirani zabwino.”+ 21  Poyankha, anthuwo anauza Yoswa kuti: “Ayi! Ife tizitumikira Yehova.”+ 22  Pamenepo Yoswa anauza anthuwo kuti: “Inu ndinu mboni mwa kufuna kwanu,+ zotsimikizira kuti mwasankha nokha kutumikira Yehova.”+ Ndiyeno anthuwo anati: “Inde! Ndife mboni.” 23  “Tsopano chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu,+ ndipo tembenuzirani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.” 24  Ndiyeno anthuwo anamuyankha Yoswa kuti: “Tizitumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mawu ake!”+ 25  Pa tsikulo, Yoswa anachita pangano ndi anthuwo ndi kuwaikira lamulo ndi chigamulo+ ku Sekemu. 26  Ndiyeno Yoswa analemba mawu amenewa m’buku la chilamulo cha Mulungu.+ Atatero, anatenga mwala waukulu+ ndi kuuika pansi pa mtengo waukulu kwambiri+ umene uli pafupi ndi malo opatulika a Yehova. 27  Kenako Yoswa anauza anthu onsewo kuti: “Taonani! Mwala uwu ukhala mboni yotsutsana nafe,+ chifukwa mwalawu wamva mawu onse amene Yehova walankhula kwa ife, ndipo ukhala mboni kwa inu kuti musadzakane Mulungu wanu.” 28  Atatero, Yoswa anauza anthuwo kuti azipita, aliyense kucholowa chake.+ 29  Patapita nthawi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 30  Choncho anamuika m’manda m’gawo la cholowa chake ku Timinati-sera,+ kudera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. 31  Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira,+ omwe ankadziwa ntchito zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.+ 32  Mafupa a Yosefe,+ amene ana a Isiraeli anabweretsa kuchokera ku Iguputo anawaika m’manda ku Sekemu, pamalo amene Yakobo anagula kwa ana a Hamori,+ tate wa Sekemu. Malowo anawagula ndi ndalama zasiliva zokwana 100,+ ndipo anakhala a ana a Yosefe monga cholowa chawo.+ 33  Nayenso Eleazara mwana wa Aroni anamwalira.+ Choncho anamuika m’manda m’phiri la Pinihasi mwana wake,+ limene anapatsidwa m’dera lamapiri la Efuraimu.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mawu ake enieni, “m’choonadi.”