Yoswa 23:1-16

23  Tsopano Yoswa anali atakalamba ndiponso anali ndi zaka zambiri.+ Apa n’kuti patapita masiku ambiri kuchokera pamene Yehova anapatsa Aisiraeli mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira.  Pa nthawiyo, Yoswa anaitana Aisiraeli onse+ ndi akulu awo, omwe anali atsogoleri awo, oweruza awo, ndi akapitawo awo,+ n’kuwauza kuti: “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.  Inuyo mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu anachitira mitundu yonse chifukwa cha inu.+ Yehova Mulungu wanu ndiye anali kukumenyerani nkhondo.+  Taonani, ndinakupatsani malo a mitundu yonse imene yatsalayi mwa kuchita maere.+ Ndinakupatsaninso malo a mitundu imene ndinaiwononga+ kuchokera kumtsinje wa Yorodano, mpaka kolowera dzuwa, ku Nyanja Yaikulu, monga cholowa cha mafuko anu.+  Yehova Mulungu wanu ndiye anali kuwathamangitsa pamaso panu,+ ndipo anawapitikitsa chifukwa cha inu. Pamenepo, inu munatenga malo awo monga mmene Yehova Mulungu wanu anakulonjezerani.+  “Tsopano khalani olimba mtima kwambiri,+ kuti musunge ndi kuchita zonse zimene zinalembedwa m’buku+ la chilamulo cha Mose, posapatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere.+  Ndiponso musayanjane ndi mitundu+ imene yatsala pakati panu. Musamatchule mayina a milungu yawo+ kapena kulumbirira pa milunguyo,+ ndipo musamaitumikire kapena kuigwadira.+  Koma mamatirani+ Yehova Mulungu wanu monga mmene mwakhala mukuchitira kufikira lero.  Yehova adzapitikitsa mitundu ikuluikulu ndiponso yamphamvu kuichotsa pamaso panu.+ (Kufikira lero, palibe munthu ngakhale mmodzi amene wakwanitsa kulimbana nanu.)+ 10  Munthu mmodzi yekha wa inu adzathamangitsa anthu 1,000,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye akukumenyerani nkhondo,+ monga mmene anakulonjezerani.+ 11  Muzikonda Yehova Mulungu wanu,+ ndipo potero tetezani miyoyo yanu nthawi zonse.+ 12  “Koma mukatembenuka+ n’kumamatira zotsala za anthu awa a mitundu ina,+ amene atsala pakati panuwa, kumakwatirana nawo,+ n’kumakhala pakati pawo, iwonso n’kumakhala pakati panu, 13  dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzaleka kuwapitikitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu.+ Adzakhalanso ngati zokubayani* m’mbali mwanu komanso ngati zitsotso m’maso mwanu, kufikira mutatheratu padziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 14  “Tsopano taonani! Ine ndatsala pang’ono kufa.+ Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+ 15  Mawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu analankhula akwaniritsidwa pa inu,+ momwemonso Yehova adzakwaniritsa pa inu mawu onse oipa, kufikira atakufafanizani kukuchotsani padziko labwinoli, limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 16  Adzatero chifukwa chakuti mwaphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu limene anakulamulani, ndiponso chifukwa chakuti mwapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani+ ndipo mudzatha mwamsanga padziko labwino limene iye anakupatsani.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kulasa.”