Yoswa 22:1-34

22  Pa nthawi imeneyo, Yoswa anaitana Arubeni, Agadi ndi hafu ya fuko la Manase,+  n’kuwauza kuti: “Inu mwasunga zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani,+ ndiponso mwamvera mawu anga m’zonse zimene ndakulamulirani.+  Simunawasiye abale anu masiku onsewa+ kufikira lero, ndipo mwasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu.+  Tsopano Yehova Mulungu wanu wapatsa abale anu mpumulo monga momwe anawalonjezera.+ Chotero bwererani, mupite kumahema anu m’dziko lanu, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani kutsidya lina la Yorodano.+  Koma mukaonetsetse kuti mukusunga malamulo+ ndi Chilamulo chimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani. Mukachite zimenezi mwa kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda m’njira zake zonse,+ kusunga malamulo ake,+ kum’mamatira,+ ndiponso kum’tumikira+ ndi mtima wanu wonse+ ndiponso moyo wanu wonse.”+  Atatero, Yoswa anawadalitsa+ n’kuwauza kuti azipita kumahema awo.  Mose anali atapatsa hafu ya fuko la Manase cholowa ku Basana.+ Hafu ina ya fukolo, Yoswa anaipatsa cholowa pamodzi ndi abale awo kutsidya lina la Yorodano kumadzulo.+ Ndipo Yoswa anawadalitsa pamene anawauza kuti azipita kumahema awo.  Anawauza kuti: “Bwererani kumahema anu ndi chuma chambiri ndiponso ziweto zambiri, ndi siliva, golide, mkuwa, zitsulo, ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munafunkha+ kwa adani anu n’kugawana ndi abale anu.”  Zitatero, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase, anachoka ku Silo kumene kunali ana ena a Isiraeli m’dziko la Kanani. Anapita ku Giliyadi,+ dziko lawo limene anapatsidwa ndi Mose molamulidwa ndi Yehova, ndiponso limene anakhazikikamo.+ 10  Atafika kuchigawo cha Yorodano chimene chinali m’dziko la Kanani, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase anamanga guwa lansembe m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano, ndipo guwalo+ linali lalikulu zedi. 11  Kenako ana ena a Isiraeli anauzidwa+ kuti: “Tamverani! Ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase amanga guwa lansembe m’malire a dziko la Kanani, m’chigawo cha Yorodano kumbali ya ana a Isiraeli.” 12  Ana a Isiraeli atamva zimenezi, khamu lawo lonse+ linasonkhana ku Silo+ kuti apite kukawathira nkhondo.+ 13  Kenako ana a Isiraeli anatumiza+ Pinihasi+ mwana wa wansembe Eleazara, kwa ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase, ku Giliyadi. 14  Anam’tumiza pamodzi ndi atsogoleri 10. Fuko lililonse la Isiraeli linatumiza mtsogoleri mmodzi woimira nyumba ya makolo ake. Mtsogoleri aliyense anali woimira nyumba ya bambo ake pakati pa Aisiraeli masauzande.+ 15  Anthuwo anafika kwa ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi, n’kuyamba kuwauza+ kuti: 16  “Khamu lonse la Yehova+ lati, ‘N’chifukwa chiyani mwachita zosakhulupirika+ kulakwira Mulungu wa Isiraeli? N’chifukwa chiyani lero mwatembenuka n’kusiya+ kutsatira Yehova podzimangira guwa lansembe+ kuti mupandukire Yehova? 17  Kodi cholakwa chimene tinachita ku Peori+ chatichepera? Kufikira lero, sitinadziyeretsebe ku cholakwa chimene chija, ngakhale kuti mliri unagwera khamu la Yehova.+ 18  Kodi inuyo tsopano mukufuna kubwerera n’kusiya kutsatira Yehova? Mukapandukira Yehova lero, ndiye kuti mawa adzakwiyira khamu lonse la Isiraeli.+ 19  Ngati n’zoona kuti dziko lanu n’lodetsedwa,+ wolokerani kudziko la Yehova+ kumene kuli chihema chopatulika cha Yehova,+ mukakhazikike pakati pathu. Koma musapandukire Yehova, ndipo musachititse ifeyo kupanduka chifukwa cha guwa lansembe limene mwamangali, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu.+ 20  Kodi Akani+ mwana wa Zera sanachite zosakhulupirika pa chinthu choyenera kuwonongedwa? Kodi mkwiyo sunagwere khamu lonse la Isiraeli?+ Komatu iye sanafe yekha chifukwa cha cholakwa chakecho.’”+ 21  Atamva zimenezi, ana a Rubeni, ana a Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase anayankha+ atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, kuti:+ 22  “Wamphamvu,+ Mulungu,+ Yehova,+ Wamphamvu, Mulungu, Yehova, iye akudziwa,+ ndipo nayenso Isiraeli adziwa.+ Ngati tachita zimenezi chifukwa chopanduka+ ndiponso chifukwa cha kusakhulupirika pamaso pa Yehova,+ musatisiye amoyo lero. 23  Ngati tadzimangira guwa lansembe kuti titembenuke n’kusiya kutsatira Yehova, ndipo ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zopsereza ndi nsembe zambewu,+ ndiponso ngati timafuna kuti tiziperekerapo nsembe zachiyanjano, Yehova afufuza yekha.+ 24  Koma ife tinamanga guwa lansembeli chifukwa choda nkhawa kuti, ‘Tsiku lina m’tsogolo muno ana anu adzauza ana athu kuti: “Inu muli naye chiyani Yehova Mulungu wa Isiraeli? 25  Yehova waika malire pakati pa ife ndi inuyo ana a Rubeni ndi ana a Gadi. Malire ake ndi mtsinje wa Yorodano. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.”+ Chotero ana anu adzachititsa ana athu kusiya kuopa Yehova.’+ 26  “Choncho tinati, ‘Tsopano tiyeni tichitepo kanthu kumbali yathu mwa kumanga guwa, osati loperekerapo zopereka kapena nsembe zopsereza, 27  koma kuti likhale mboni pakati pa ife+ ndi inu ndi mibadwo yobwera pambuyo pathu. Guwalo likhale mboni yakuti tidzatumikira Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, nsembe zachiyanjano ndi nsembe zina,+ kuti tsiku lina m’tsogolo ana anu asadzanene kwa ana athu kuti: “Inu mulibe gawo mwa Yehova.”’ 28  Chotero tinati, ‘Akadzanena zimenezi kwa ife ndi kwa mibadwo yathu m’tsogolo, ifenso tidzati: “Taonani chifaniziro cha guwa lansembe la Yehova chimene makolo athu anamanga, osati choperekerapo zopereka kapena nsembe zopsereza, koma monga mboni ya pakati pa ife ndi inu.”’ 29  N’zosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova+ mwadala, n’kuleka kutsatira Yehova mwa kumanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa chihema chake chopatulika!”+ 30  Wansembe Pinihasi,+ atsogoleri a khamu la Aisiraeli+ kapena kuti atsogoleri a masauzande a Aisiraeli amene anali naye, atamva mawu amene ana a Rubeni, ana a Gadi ndi ana a Manase ananena, anakhutira nawo mawuwo. 31  Ndiyeno Pinihasi mwana wa wansembe Eleazara, anauza ana a Rubeni, ana a Gadi ndi ana a Manase, kuti: “Lero tadziwa kuti Yehova ali pakati pathu+ chifukwa simunapandukire Yehova. Tsopano mwalanditsa ana a Isiraeli m’dzanja la Yehova.”+ 32  Pamenepo, Pinihasi mwana wa wansembe Eleazara ndi atsogoleri aja, anachoka kwa ana a Rubeni ndi ana a Gadi m’dziko la Giliyadi, n’kubwerera+ kwa ana ena a Isiraeli kudziko la Kanani. Kumeneko, iwo anawafotokozera zimene ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena.+ 33  Ana a Isiraeli atamva mawuwo, anakhutira nawo ndipo anatamanda Mulungu.+ Ndipo sananenenso zopita kukamenyana ndi ana a Rubeni ndi ana a Gadi, ndi kuwononga dziko limene iwo anali kukhalamo. 34  Ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha dzina guwalo.* Iwo anati, “Guwali ndi mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu woona.”+

Mawu a M'munsi

Guwalo ayenera kuti analitcha dzina lakuti, “Mboni.”