Yoswa 21:1-45

21  Tsopano atsogoleri a mabanja a Alevi, anapita kwa wansembe Eleazara,+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli.  Analankhula nawo ku Silo+ m’dziko la Kanani, kuti: “Kudzera mwa Mose, Yehova analamula kuti tipatsidwe mizinda yoti tizikhalamo, pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayo, oti tizidyetserako ziweto zathu.”+  Choncho ana a Isiraeli pomvera lamulo la Yehova, anapatsa Alevi+ mizindayo ndi malo ake odyetserako ziweto, kuchokera pa cholowa chawo.+  Atachita maere, maerewo anagwera mabanja a Akohati.+ Choncho mizinda 13 inakhala ya ana a wansembe Aroni, omwe anali Alevi. Mizinda yake inachokera m’mafuko a Yuda,+ Simiyoni,+ ndi Benjamini.+  Anachita maere ena, ndipo ana a Kohati+ amene anatsala anawapatsa mizinda 10 yochokera m’mabanja a fuko la Efuraimu,+ Dani,+ ndi hafu ya fuko la Manase.+  Anachitanso maere, ndipo ana a Gerisoni+ anapatsidwa mizinda 13 yochokera m’mabanja a fuko la Isakara,+ Aseri,+ Nafitali,+ ndi hafu ya fuko la Manase ku Basana.+  Ana a Merari+ anapatsidwa mizinda 12 yochokera m’fuko la Rubeni,+ Gadi,+ ndi Zebuloni,+ potsata mabanja awo.  Chotero ana a Isiraeli anapatsa Alevi mizinda imeneyi ndi malo ake odyetserako ziweto,+ mwa kuchita maere.+ Anachita zimenezi monga mmene Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose.+  Ana a Isiraeli anapereka mizinda, kuchokera m’fuko la ana a Yuda ndi fuko la ana a Simiyoni. Mizindayo anachita kuitchula mayina.+ 10  Mizinda yotsatirayi inakhala ya ana a Aroni ochokera m’mabanja a Akohati, omwe anali ana a Levi, chifukwa maere oyamba anagwera iwowa.+ 11  Anawapatsa Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali tate wa Anaki.)+ Mzindawu, pamodzi ndi malo ouzungulira odyetserako ziweto, unali m’dera lamapiri la Yuda.+ 12  Malo ozungulira mzindawo ndi midzi yake, anawapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune kuti akhale ake.+ 13  Ana a wansembe Aroni anawapatsa mzinda wothawirako munthu+ amene wapha mnzake,+ wa Heburoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 14  Yatiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Esitemowa+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 15  Holoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 16  Aini+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yuta+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beti-semesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda 9, kuchokera m’mafuko awiri amenewa. 17  Kuchokera m’fuko la Benjamini, anawapatsa Gibeoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Geba+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 18  Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Alimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 19  Mizinda yonse ya ansembe, ana a Aroni,+ inalipo 13 ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 20  Mabanja a ana a Kohati, kapena kuti Alevi otsala pa ana a Kohati, anapatsidwa mizinda yochokera m’fuko la Efuraimu. Iwo anapatsidwa mizindayi pambuyo pochita maere.+ 21  Motero anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Sekemu,+ ndi malo ake odyetserako ziweto+ m’dera lamapiri la Efuraimu. Anawapatsanso Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 22  Kibizaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 23  Kuchokera m’fuko la Dani, anawapatsa Eliteke ndi malo ake odyetserako ziweto, Gebetoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 24  Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Gati-rimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 25  Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anawapatsa Taanaki+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Gati-rimoni ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri. 26  Mizinda yonse pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto, imene mabanja a ana otsala a Kohati anapatsidwa, inalipo 10. 27  Ana a Gerisoni+ a m’mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda kuchokera ku hafu ya fuko la Manase.+ Anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Golani+ ku Basana, ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Beesitera+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Inalipo mizinda iwiri. 28  Kuchokera m’fuko la Isakara,+ anawapatsa Kisioni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 29  Yarimuti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Eni-ganimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 30  Kuchokera m’fuko la Aseri,+ anawapatsa Misali+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Abidoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 31  Helikati+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 32  Kuchokera m’fuko la Nafitali,+ anawapatsa mzinda wothawirako+ munthu amene wapha mnzake,+ wa Kedesi,+ ku Galileya ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Hamoti-dori+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Karitani ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu. 33  Mizinda yonse ya Agerisoni potsata mabanja awo inalipo 13, ndi malo ake odyetserako ziweto. 34  Kuchokera m’fuko la Zebuloni,+ mabanja a ana a Merari,+ amene ndi Alevi otsala, anapatsidwa Yokineamu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Karita ndi malo ake odyetserako ziweto, 35  Dimena+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Nahalala+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 36  Kuchokera m’fuko la Rubeni,+ anawapatsa Bezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 37  Kademoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Mefaata+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 38  Kuchokera m’fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi,+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 39  Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, ndiponso Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Yonse pamodzi inalipo mizinda inayi. 40  Ana a Merari,+ omwe anatsala pa mabanja a Alevi, anapatsidwa mizinda yokwana 12 potsata mabanja awo, mwa kuchita maere. 41  Mizinda yonse ya Alevi m’dziko limene ana a Isiraeli anapatsidwa inalipo 48,+ pamodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 42  Mzinda uliwonse pa mizinda imeneyi unazunguliridwa ndi malo odyetserako ziweto. Ndi mmene mizinda yonseyi inalili.+ 43  Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,+ ndipo iwo analanda+ dzikolo n’kumakhalamo. 44  Kuwonjezera apo, Yehova anawapatsa mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira+ makolo awo. Panalibe ngakhale mdani mmodzi pa adani awo onse amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse m’manja mwawo.+ 45  Palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.+

Mawu a M'munsi