Yoswa 20:1-9

20  Kenako Yehova anauza Yoswa kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako+ mogwirizana ndi zimene ndinakuuzani kudzera mwa Mose.  Mizindayo ntchito yake ikhale yoti wopha munthu+ mwangozi azithawirako pothawa wobwezera magazi.+  Azithawira+ kumzinda umodzi mwa mizindayi n’kukaima pachipata+ cholowera mumzindawo. Akatero azifotokoza nkhani yake kwa akulu+ a mzindawo. Akuluwo amulandire n’kumupatsa malo mumzindamo kuti azikhala nawo limodzi.  Ngati wobwezera magazi atam’thamangitsa, akuluwo asapereke wopha munthuyo m’manja mwa wobwezera magaziyo,+ chifukwa iye sanaphe munthu mnzakeyo mwadala, ndiponso sankadana naye.+  Munthuyo azikhala mumzindawo mpaka atakaonekera pamaso pa oweruza,+ komanso mpaka mkulu wa ansembe amene alipo pa nthawiyo atafa.+ Izi zikachitika, wopha munthuyo akhoza kubwerera kwawo,+ n’kukalowa m’nyumba mwake, mumzinda momwe anathawamo muja.’”  Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.  Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.  Imeneyi inali mizinda imene inasankhidwa kuti ana a Isiraeli onse ndi alendo okhala pakati pawo, azithawirako akapha munthu mwangozi,+ kuti asaphedwe ndi wobwezera magazi mpaka akaonekere pamaso pa oweruza.+

Mawu a M'munsi