Yoswa 2:1-24

2  Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatumiza amuna awiri mwachinsinsi monga azondi kuchokera ku Sitimu.+ Anawalangiza kuti: “Pitani, mukazonde dzikolo ndi mzinda wa Yeriko.” Chotero iwo anapita n’kukafika kunyumba ya mayi wina yemwe anali hule, dzina lake Rahabi,+ n’kukhala kumeneko.  Kenako mfumu ya Yeriko inauzidwa kuti: “Taonani! Amuna ochokera kwa ana a Isiraeli alowa mumzinda wathu usiku uno kudzafufuza dziko lathu.”  Mfumu ya Yeriko itamva zimenezo inatumiza anthu kukauza Rahabi kuti: “Tulutsa amuna amene abwera kwa iwe, omwe alowa m’nyumba mwako, chifukwa abwera kudzafufuza dziko lathu lonse lino.”+  Pamenepo mayiyo anatenga amuna awiriwo n’kuwabisa. Kenako anayankha kuti: “Inde, amunawo anabweradi kwa ine, koma sindinadziwe kuti achokera kuti.  Ndipo amunawo atuluka usiku uno nthawi yotseka chipata+ itayandikira. Koma ine sindikudziwa kumene alowera. Fulumirani! Athamangireni! Muwapeza amenewo.”  (Koma iye anali atawatengera padenga,*+ ndi kuwabisa pansi pa mapesi a fulakesi* padengapo.)  Amunawo anathamangira azondi aja, cha kowolokera mtsinje wa Yorodano.+ Ndipo atangotuluka pachipata cha mzinda, nthawi yomweyo chipatacho chinatsekedwa.  Azondi aja asanagone, Rahabi anakwera padenga pamene iwo anali.  Ndipo iye anauza amunawo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.+ Ife tagwidwa ndi mantha chifukwa cha inu,+ ndipo anthu a dziko lino ataya mtima chifukwa chokuopani.+ 10  Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano. 11  Titangomva zimenezi, mitima yathu inayamba kusungunuka ndi mantha,+ ndipo mpaka pano palibe aliyense amene akulimba mtima, chifukwa choopa inu.+ Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa kumwamba ndi padziko lapansi.+ 12  Tsopano, chonde lumbirani kwa ine pali Yehova,+ kuti chifukwa choti ndakusonyezani kukoma mtima kosatha, inunso mudzasonyeza anthu a m’nyumba ya bambo anga+ kukoma mtima kosatha, ndipo mundipatse chizindikiro chodalirika.+ 13  Musadzaphe bambo anga,+ mayi anga, abale anga ndi alongo anga, limodzi ndi mabanja awo. Mudzatisiye amoyo.”+ 14  Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe m’malo mwa inu!+ Mukasunga chinsinsi cha nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dziko lino, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima kosatha, ndipo tidzakhulupirika kwa inu.”+ 15  Pambuyo pake, mkaziyo anatulutsa amunawo powatsitsa ndi chingwe pawindo, pakuti mpanda wa mzindawo unalinso khoma* la nyumba yake, ndipo nyumba yakeyo inali pampandapo.+ 16  Iye anauza amunawo kuti: “Muthawire kumapiri kuti amene akukusakani aja asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu, mpaka iwo atabwerako, kenako muzikapita kwanu.” 17  Amunawo anayankha kuti: “Tisungadi pangano limene iwe watilumbiritsa, ndipo tidzakhala opanda mlandu.+ 18  Tikubwera ndithu m’dziko muno! Chingwe chofiira ichi uchimangirire pawindo limene watitulutsirapo. Bambo ako ndi mayi ako, abale ako ndi alongo ako, ndi onse a m’nyumba ya bambo ako, uwasonkhanitse kuti adzakhale m’nyumba mwako.+ 19  Aliyense amene adzatuluke pakhomo la nyumba yako kupita panja,+ magazi ake adzakhala pamutu pake. Ife tidzakhala opanda mlandu. Koma ngati aliyense amene adzakhalebe limodzi nawe m’nyumbamu adzaphedwe, magazi ake adzakhale pamutu pathu. 20  Ndipo ngati ungaulule nkhaniyi,+ tidzakhalanso opanda mlandu pa pangano limene watilumbiritsali.” 21  Pamenepo mkaziyo anati: “Zikhale monga mwanenera.” Atatero anawauza kuti azipita, ndipo iwo ananyamuka. Kenako mkaziyo anamanga chingwe chofiira chija pawindopo. 22  Chotero amuna aja anatuluka, nakafika kumapiri kuja. Anakhala kumeneko masiku atatu mpaka owasaka aja atabwerera. Owasakawo anawafunafuna mumsewu uliwonse, koma sanawapeze. 23  Amuna aja anatsika m’mapirimo, ndipo atawoloka mtsinje, anakafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Atafika, anayamba kum’fotokozera zonse zimene zinawachitikira. 24  Iwo anauza Yoswa kuti: “Yehova wapereka dziko lonselo m’manja mwathu.+ Ndipo anthu onse a m’dzikomo akuchita mantha chifukwa cha ife.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “patsindwi.”
Fulakesi ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”