Yoswa 15:1-63

15  Gawo+ la fuko la ana a Yuda potsata mabanja awo linkafika kumalire a Edomu,+ ndi kuchipululu cha Zini,+ mpaka kothera kwa Negebu,+ kum’mwera.  Malire awo a kum’mwera ankayambira kumapeto kwa Nyanja Yamchere,+ kugombe lake la kum’mwera.  Malirewo analowera kum’mwera kuchitunda cha Akirabimu+ n’kukafika ku Zini.+ Kenako anakwera kuchokera kum’mwera kupita ku Kadesi-barinea,+ n’kukadutsa ku Hezironi mpaka ku Adara, n’kuzungulira kukafika ku Karika.  Ndiyeno anapitirira kukafika ku Azimoni+ mpaka kuchigwa cha Iguputo,+ n’kukathera kunyanja. Amenewa ndiwo anali malire awo a kum’mwera.  Malire a kum’mawa anali Nyanja Yamchere mpaka pamene mtsinje wa Yorodano umathirira m’nyanjayi. Malire a gawoli kumpoto, anakhota pagombe pamene mtsinje wa Yorodano umathirira m’nyanjayi.+  Malirewo anapitirira mpaka ku Beti-hogila+ n’kukadutsa kumpoto kwa Beti-araba,+ n’kukafika kumwala wa Bohani,+ mwana wa Rubeni.  Anakafika ku Debiri kuchigwa cha Akori+ n’kukhotera kumpoto cha ku Giligala,+ patsogolo pa chitunda cha Adumi, kum’mwera kwa chigwa cha mtsinje. Malirewo anapitirira n’kukafika kumadzi a Eni-semesi,+ n’kukathera ku Eni-rogeli.+  Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kum’mwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyang’anizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai,+ kumapeto kwa chigwacho.  Kuchokera pamwamba pa phirilo, malirewo anakafika kukasupe wa madzi a Nafitoa,+ n’kupitirira mpaka kumizinda ya m’mphepete mwa phiri la Efuroni. Anapitirirabe mpaka ku Baala,+ kutanthauza Kiriyati-yearimu.+ 10  Kuchokera ku Baala, malirewo anazungulira chakumadzulo kulowera kuphiri la Seiri, n’kukadutsa pamalo otsetsereka a phiri la Yearimu kumpoto, kutanthauza Kesaloni. Ndiyeno anatsetserekera ku Beti-semesi,+ n’kukafika ku Timuna.+ 11  Malirewo anakafika kumalo otsetsereka otchedwa Ekironi+ kumpoto, n’kukadutsa ku Sikeroni. Anapitirira mpaka kuphiri la Baala kukafika ku Yabineeli, n’kukathera kunyanja. 12  Malire a kumadzulo anali Nyanja Yaikulu+ ndi gombe lake. Amenewa ndiwo anali malire onse a ana a Yuda potsata mabanja awo. 13  Kalebe+ mwana wa Yefune anam’patsa gawo lake pakati pa ana a Yuda pomvera lamulo la Yehova kwa Yoswa. Anam’patsa Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni.+ (Ariba anali tate wa Anaki.) 14  Choncho Kalebe anapitikitsa ana atatu a Anaki+ kuderalo. Anawo anali Sesai,+ Ahimani, ndi Talimai,+ obadwa kwa Anaki.+ 15  Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a ku Debiri.+ (Zimenezi zisanachitike, Debiri ankatchedwa Kiriyati-seferi.)+ 16  Kenako Kalebe anati: “Aliyense amene agonjetse mzinda wa Kiriyati-seferi n’kuulanda, ndithu ndim’patsa mwana wanga Akisa,+ kuti akhale mkazi wake.” 17  Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ m’bale wake wa Kalebe, analanda mzindawo. Chotero Kalebe anam’patsa Akisa,+ mwana wake, kuti akhale mkazi wake. 18  Akisa ali pabulu pa ulendo wopita kunyumba, anakakamiza Otiniyeli kuti apemphe malo kwa Kalebe bambo ake. Ndiyeno Akisa anawomba m’manja kuitana bambo ake, ndipo Kalebe atamva, anam’funsa kuti: “Ukufuna chiyani?”+ 19  Iye anayankha kuti: “Ndidalitseni, poti mwandipatsa malo a kum’mwera, tsopano mundipatsenso Guloti-maimu.”* Pamenepo Kalebe anam’patsa Guloti Wakumtunda ndi Guloti Wakumunsi.+ 20  Ichi chinali cholowa+ cha fuko la ana a Yuda,+ potsata mabanja awo. 21  Mizinda ya kumapeto kwa gawo la fuko la ana a Yuda, chakumalire ndi Edomu+ kum’mwera, inali Kabizeeli,+ Ederi, Yaguri, 22  Kina, Dimona, Adada, 23  Kedesi, Hazori, Itinani, 24  Zifi, Telemu,+ Bealoti, 25  Hazori-hadata, Kerioti-hezironi, kutanthauza Hazori, 26  Amamu, Sema, Molada,+ 27  Hazara-gada, Hesimoni, Beti-peleti,+ 28  Hazara-suali,+ Beere-seba,+ Bizioti, 29  Baala,+ Iimu, Ezemu,+ 30  Elitoladi, Kesili, Horima,+ 31  Zikilaga,+ Madimana, Sanasana, 32  Lebaoti, Silihimu, Aini,+ ndi Rimoni.+ Mizinda yonse inalipo 29, pamodzi ndi midzi yake. 33  Ku Sefela+ kunali Esitaoli,+ Zora,+ Asina, 34  Zanowa,+ Eni-ganimu, Tapuwa, Enamu, 35  Yarimuti,+ Adulamu,+ Soko,+ Azeka,+ 36  Saaraimu,+ Aditaimu, Gedera, ndi Gederotaimu. Mizinda 14 ndi midzi yake. 37  Zenani, Hadasha, Migidala-gadi, 38  Dilani, Mizipe, Yokiteeli, 39  Lakisi,+ Bozikati,+ Egiloni,+ 40  Kaboni, Lamamu, Kitilisi, 41  Gederoti, Beti-dagoni, Naama, ndi Makeda.+ Mizinda 16 ndi midzi yake. 42  Libina,+ Eteri,+ Asani, 43  Ifita, Asina, Nezibi, 44  Keila,+ Akizibu,+ ndi Maresha.+ Mizinda 9 ndi midzi yake. 45  Ekironi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe. 46  Kuchokera ku Ekironi kulowera chakumadzulo, malo onse amene ali m’mphepete mwa Asidodi ndi midzi yake. 47  Asidodi+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe, Gaza+ pamodzi ndi midzi yake yozungulira, ikuluikulu ndi ing’onoing’ono yomwe, mpaka kukafika kuchigwa cha Iguputo, ndi ku Nyanja Yaikulu pamodzi ndi dera la m’mphepete mwa nyanjayi.+ 48  Kudera lamapiri kunali Samiri, Yatiri,+ Soko, 49  Dana, Kiriyati-sana, kutanthauza Debiri, 50  Anabi, Esitemo,+ Animu, 51  Goseni,+ Holoni, ndi Gilo.+ Mizinda 11 ndi midzi yake. 52  Arabu, Duma, Esana, 53  Yanimu, Beti-tapuwa, Apeka, 54  Humita, Kiriyati-ariba, kutanthauza Heburoni,+ ndi Ziori. Mizinda 9 ndi midzi yake. 55  Maoni,+ Karimeli, Zifi,+ Yuta, 56  Yezereeli, Yokideamu, Zanowa, 57  Kayini, Gibea, ndi Timuna.+ Mizinda 10 ndi midzi yake. 58  Haluli, Beti-zuri, Gedori, 59  Maaratu, Beti-anotu, ndi Elitekoni. Mizinda 6 ndi midzi yake. 60  Kiriyati-baala,+ kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ ndi Raba. Mizinda iwiri ndi midzi yake. 61  Kuchipululu kunali Beti-araba,+ Midini, Sekaka, 62  Nibisani, Mzinda wa Mchere, ndi Eni-gedi.+ Mizinda 6 ndi midzi yake. 63  Ana a Yuda analephera kupitikitsa+ Ayebusi+ omwe anali kukhala ku Yerusalemu,+ moti Ayebusi akukhalabe limodzi ndi ana a Yuda ku Yerusalemu mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “Guloti-maimu” amatanthauza “Zigwa za Madzi.”