Yoswa 13:1-33

13  Tsopano Yoswa anali atakalamba, ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Choncho Yehova anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba ndipo uli ndi zaka zambiri, koma dziko loti lilandidwe likadali lalikulu.+  Dziko limene latsala ndi ili:+ Madera onse a Afilisiti+ ndi madera onse a Agesuri.+  (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo kum’mawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi,+ ankalitcha dziko la Akanani.)+ Madera a Afilisitiwa akulamulidwa ndi olamulira ogwirizana asanu.+ Maderawo ndi Gaza,+ Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ komanso Aavi+ akukhala komweko.  Kum’mwera kwatsala dziko lonse la Akanani. Patsalanso mzinda wa Asidoni+ wotchedwa Meara, mpaka kukafika ku Afeki kumalire a Aamori,  dziko la Agebala+ ndiponso dziko lonse la Lebanoni, kotulukira dzuwa, kuyambira ku Baala-gadi+ m’munsi mwa phiri la Herimoni mpaka kumalire ndi Hamati.+  Ine ndidzapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli anthu onse okhala kudera lamapiri, kuchokera ku Lebanoni+ mpaka ku Misirepotu-maimu,+ ndidzapitikitsa Asidoni onse.+ Iweyo ungopereka dzikoli kwa ana a Isiraeli+ kuti likhale cholowa chawo monga mmene ndinakulamulira.+  Dzikoli uligawe kwa mafuko 9 ndiponso kwa hafu ya fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”+  Mose mtumiki wa Yehova anapereka cholowa kwa hafu ina ya fuko la Manase, kwa Arubeni ndi kwa Agadi, kutsidya la kum’mawa kwa Yorodano.+  Cholowa chawo chinayambira kumzinda wa Aroweli+ umene uli m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni,+ ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho, kuphatikizapo malo onse okwererapo a Medeba+ mpaka kukafika ku Diboni.+ 10  Anawapatsanso mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ku Hesiboni, mpaka kumalire ndi ana a Amoni.+ 11  Anapatsidwanso dera la Giliyadi, la Agesuri,+ la Amaakati, phiri lonse la Herimoni,+ ndi dera lonse la Basana+ mpaka ku Saleka.+ 12  Mafukowa anatenganso dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi+ mfumu ya Basana, imene inali kulamulira ku Asitaroti ndi ku Edirei.+ Mfumu Ogi anali mmodzi mwa Arefai otsala.+ Mose anagonjetsa anthu onsewa ndi kuwapitikitsa.+ 13  Koma ana a Isiraeli sanapitikitse+ Agesuri ndi Amaakati. Ndipo iwo+ akukhalabe pakati pawo kufikira lero. 14  Fuko la Alevi lokha ndi limene sanalipatse cholowa cha malo.+ Cholowa chawo ndicho nsembe zotentha ndi moto+ zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga mmene anawalonjezera.+ 15  Tsopano Mose anagawira dziko ana a Rubeni potsata mabanja awo. 16  Dziko lawo linayambira ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikoli linaphatikizapo malo onse okwererapo apafupi ndi Medeba,+ 17  Hesiboni,+ ndi midzi yake yonse+ imene inali m’malo okwererapowo. Linaphatikizaponso Diboni,+ Bamoti-baala,+ Beti-baala-meoni,+ 18  Yahazi,+ Kademoti,+ Mefaata,+ 19  Kiriyataimu,+ Sibima,+ Zereti-sahara, malo amene anali m’phiri la kuchigwa, 20  Beti-peori, dera lotsetsereka la ku Pisiga,+ Beti-yesimoti,+ 21  mizinda yonse ya m’malo okwererapo,+ ndiponso dziko lonse la Sihoni mfumu ya Aamori imene inali kulamulira ili ku Hesiboni.+ Mfumu imeneyi Mose anaipha+ limodzi ndi atsogoleri a ku Midiyani, Evi, Rekemu, Zuri, Hura, ndi Reba.+ Amenewa anali mafumu omwe anali pansi pa Sihoni ndipo anali kukhala m’dzikolo. 22  Pakati pa anthu amene ana a Isiraeli anawapha ndi lupanga, panali Balamu mwana wa Beori,+ wolosera zam’tsogolo+ uja. 23  Malire a ana a Rubeni anali mtsinje wa Yorodano. Limeneli ndilo gawo la ana a Rubeni+ limene anapatsidwa potsata mabanja awo. Iwo anapatsidwa mizinda ndi midzi ya kumeneko kuti ikhale cholowa chawo. 24  Kenako Mose anagawira dziko fuko la ana a Gadi potsata mabanja awo.+ 25  Gawo lawo linayambira kumzinda wa Yazeri,+ mizinda yonse ya ku Giliyadi,+ ndi hafu ya dziko la ana a Amoni,+ mpaka kukafika ku Aroweli+ kufupi ndi Raba.+ 26  Kuchokera ku Hesiboni+ linakafika ku Ramati-mizipe ndi ku Betonimu, ndiponso kuchokera ku Mahanaimu+ mpaka kumalire ndi Debiri.+ 27  Gawo lawolo linaphatikizaponso mizinda ya m’chigwa ya Beti-harana,+ Beti-nimira,+ Sukoti,+ Zafoni, ndi mbali yotsala ya dziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni.+ Mtsinje wa Yorodano ndiwo unali malire awo mpaka kunyanja ya Kinereti.+ Gawo lawo linali kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. 28  Ili ndilo dziko limene ana a Gadi+ anapatsidwa monga cholowa chawo potsata mabanja awo. Anapatsidwa mizinda ya kumeneko ndi midzi yake yomwe. 29  Kenako Mose anapereka dziko kwa hafu ya fuko la Manase potsata mabanja awo, ndipo dzikolo linakhala la ana a Manase.+ 30  Gawo lawo linayambira ku Mahanaimu+ kuphatikizapo dera lonse la Basana,+ ndi dziko lonse limene linali kulamulidwa ndi Ogi mfumu ya Basana, ndiponso midzi yonse ing’onoing’ono ya Yairi+ ku Basana. Gawo lawoli linali ndi matauni 60 onse pamodzi. 31  Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti,+ Edirei,+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi m’dziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri potsata mabanja awo. 32  Limeneli ndilo dziko limene Mose anawapatsa kuti likhale cholowa chawo, pamene anali ku Yeriko, kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano m’chipululu cha Mowabu, kum’mawa.+ 33  Fuko la Alevi, Mose sanalipatse cholowa cha malo.+ Yehova Mulungu wa Isiraeli ndiye cholowa chawo, monga mmene anawalonjezera.+

Mawu a M'munsi